BAIBULO - Akamaihd.net

16
34567 Na. 1 2016 N’ZOTHEKA KUMVETSETSA BAIBULO

Transcript of BAIBULO - Akamaihd.net

34567Na. 1 2016

N’ZOTHEKAKUMVETSETSABAIBULO

34567Na. 1 2016

N’ZOTHEKAKUMVETSETSABAIBULO

Kodi mufuna kudziwa za-mbili kapena kuphunzilaBaibo kunyumba kwanukwaulele?

Pitani pa webusaiti yathu yawww.jw.org kapena tumizanipempho lanu mwakugwilitsilanchito adilesi yoyenela pa maa-dilesi amene ali pansi awa.

Ya ku SOUTH AFRICA:Jehovah’s WitnessesPrivate Bag X2067Krugersdorp1740

Ya ZAMBIA:P.O. Box 3345910101 Lusaka

Ngati mufuna maadilesi onse,onani www.jw.org/nya/contanct.

˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙

MAGAZINI ya Nsanja ya Mlondaimalemekeza Yehova Mulungu, amenendi Wolamulila wa cilengedwe conse.Imalimbikitsa anthu ndi uthengawabwino wakuti Ufumu wa Mulunguposacedwapa udzacotsa zoipa zonsendi kusintha dziko lapansi kukhalapaladaiso. Imalimbikitsa anthukukhulupilila Yesu Kristu ameneanatifela kuti tidzapeze moyo wosatha,ndipo panthawi ino iye akulamulilamonga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.Magaziniyi yakhala ikufalitsidwakuyambila mu 1879 ndipo si yandale.Mfundo zake zonse n’zocokela m’Baibo.

The Watchtower (ISSN 0043-1087) is publishedsemimonthly by Watchtower Bible and TractSociety of New York, Inc.; L. Weaver, Jr.,President; G. F. Simonis, Secretary-Treasurer;25 Columbia Heights, Brooklyn, NY 11201-2483,and printed by Watch Tower Bible and TractSociety of South Africa NPC, 1 Robert BroomDrive East, Rangeview, Krugersdorp, 1739.� 2015 Watch Tower Bible and Tract Societyof Pennsylvania. Printed in South Africa.

Magazini iyi si yogulitsa. Colinga cake ndi kuthandi-za pa nchito yophunzitsa Baibo imene imacitikapadziko lonse lapansi. Zopeleka zaufulu n’zimenezimathandiza kupititsa patsogolo nchito imeneyi.Baibo imene tasewenzetsa ndi Baibulo la Dziko La-tsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngatitaonetsa ina. Komabe, masipeling’i a Cinyanjam’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku loche-dwa A Unified Standard Orthography forSouth-Central African Languages.

Cinyengo Kodi Cidzatha? 8

Kodi Mudziwa? 11

Tsanzilani Cikhulupililo Cao“Mwana Wanga Wokondedwa ndi Wokhulupilikamwa Ambuye” 12

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo 16

34567 Magazini a Nsanja ya Mlonda Okwana:52,946,000 Amasindikizidwa M’ZINENELO 251 Na. 1 2016������������������������������������������������������������������������������������������������������������

NKHANI YA PACIKUTO

NKHANI ZINA M’MAGAZINI INO

s��������������������������������������������������������������������������������������������ˆWELENGANI NKHANI ZINA PA INTANETI

Vol. 137, Na. 1 CINYANJA

N’zotheka Kumvetsetsa BaibuloMASAMBA 3-7

N’cifukwa Ciani Tifunika Kumvetsetsa Baibulo? 3Buku Losavuta Kumvetsetsa 4Pemphani Thandizo Kuti Mumvetsetse Baibulo 6

MAFUNSO ENA A M’BAIBULOAMENE AYANKHIDWA

Kodi Sayansi Imagwilizanandi Baibulo?(Pitani polemba kutiZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA˛ KUYANKHA MAFUNSO AM’BAIBULO)r

MUNGATENGEMAGAZINI IYI M’NJILAZOSIYANASIYANA PAINTANETI

MOYO WOKHUTIRITSA

Mmene Mungaupezere

Anthu ambili padziko lonse amalemekeza kwambili Baibulo. Nga-khale n’conco, io amadziwa nkhani zocepa za m’Baibulo mwina-nso sazidziwa n’komwe. Mfundo imeneyi ndi yoona. Mwacitsanzo,anthu mamiliyoni a ku Asia sadziwa zimene Baibulo limakamba.N’cimodzimodzinso ndi anthu ambili a m’maiko amene Baibulo ndilofala kwambili.Mwina mungadzifunse kuti: N’cifukwa ciani ndifunika kumvetse-

tsa Baibulo? Kumvetsetsa buku lopatulika limeneli, kudzakuthandi-zani kucita zotsatilazi:

˙ Kukhala wokhutila ndi wacimwemwe˙ Kulimbana ndi mavuto a m’banja˙ Kulimbana ndi nkhawa za paumoyo˙ Kukhala bwino ndi anthu ena˙ Kusewenzetsa ndalama mwanzelu

Mwacitsanzo, mvelani zimene Yoshiko wa ku Japan anakamba.Iye sanali kudziwa zimene Baibulo limakamba. Conco, anaganizazoyamba kuliwelenga. Nanga panali zotsatilapo zotani? Iye anaka-mba kuti: “Baibulo landithandiza kukhala ndi umoyo waphindu ndikukhala ndi ciyembekezo cabwino ca mtsogolo. Tsopano ndili ndiumoyo wokhutilitsa.” Amit amene tamuchula kuciyambi kwa nkha-ni ino, nayenso anayamba kuphunzila Baibulo payekha. Iye anati:“Ndinadabwa kwambili ndi uthenga wa m’Baibulo. M’bukuli, mulimfundo zothandiza kwa munthu aliyense.”Baibulo lathandiza anthu ambili kusintha umoyo wao. Bwanji osa-

liwelenga ndi kuona mmene lingakuthandizileni inuyo panokha?

NKHANI YA PACIKUTO

N’cifukwa Ciani TifunikaKumvetsetsa Baibulo?

“Baibulo ndi buku la cipembedzo lodziwika kwambili. Koma kwaanthu a Cichainizi ndi buku lacilendo ndipo n’losathandiza.”—LIN, CHINA.

“Sindimvetsetsa mabuku oyela acipembedzo canga ca Cihindu.Ndiye ndingakwanitse bwanji kumvetsetsa Baibulo Lopatulika?”—AMIT, INDIA.

“Ndimalemekeza Baibulo cifukwa ndi buku lakale, ndipo ndamva kutianthu amaligula kwambili. Koma sindinalionepo.”—YUMIKO, JAPAN.

Kuti mudziwe zambili zammene Baibulo lingaku-thandizileni, onani kabukukakuti MoyoWokhutilitsaMmene Mungaupezele,kofalitsidwa ndi Mboni zaYehova. Kapezekanso pawww.jw.org

Na. 1 2016 3

WasLifeCreated?

4 NSANJA YA MLONDA

Baibulo ndi buku lakale kwambili. Kodi lakhalapokwa zaka zingati? Baibulo linayamba kulembedwakuMiddle East zaka 3,500 zapitazo. Nthawiyo, mpa-mene ulamulilo wotsatizana wa m’banja la mafumua Cichainizi ochulidwa m’mbili yakale unayamba,komanso kutatsala zaka 1000 kuti cipembedzo caCibuda ciyambe m’dziko la India.—Onani bokosilakuti “Dziwani Izi Ponena za Baibulo.”Kuti buku likhale lothandiza ndiponso lofunika

kwambili kwa anthu, liyenela kukhala losavuta ku-mvetsetsa. Umu ndi mmene Baibulo lilili. Limape-leka mayankho ogwila mtima a mafunso ofunikakwambili.Mwacitsanzo, kodi munadzifunsapo kuti, ‘N’ci-

fukwa ciani tili ndi moyo?’ Funso limeneli lago-metsa mutu anthu kwa zaka masauzande ambili.Komabe, yankho la funso limeneli lipezeka m’ma-caputala awili oyambilila a Genesis, buku loyambam’Baibulo. M’macaputala amenewa, Baibulo limati-uza za “ciyambi,” pamene zinthu monga milalang’a-mba, nyenyezi, ndi dziko lapansi zinalengedwa zakamabiliyoni ambili zapitazo. (Genesis 1:1) Limati-uzanso mmene dziko lapansi linalengedwela kutipakhale zamoyo, mmene zamoyo zosiyanasiyana zi-nakhalilapo, ndiponso kulengedwa kwa anthu. Bai-bulo limatiuza colinga cimene Mulungu analengelazinthu zonsezi.

N’LOSAVUTA KUMVETSETSABaibulo lili ndi malangizo amene amatithandi-

za kulimbana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku. Mala-ngizo amenewo si ovuta kumvetsetsa. Onani mbaliziwili izi.Mbali yoyamba, mau a m’Baibulo ndi osavuta,

acindunji, ndiponso osangalatsa. M’malo mose-wenzetsa mau ambili ovuta kumvetsetsa, Baibu-lo lili ndi mau amene timawadziwa bwino. Mbalizovuta anazilemba m’mau amene timakamba tsikulililonse.Mwacitsanzo, Yesu anafotokoza mafanizo ambi-

li osavuta okamba za zinthu zimene anthu analikudziwa bwino. Anacita zimenezo n’colinga cakutiawafike pamtima. Ambili mwa mafanizo amenewoanawachula mu ulaliki wake wa pa phili, wolembe-dwa m’buku la m’Baibulo la Mateyu macaputala 5mpaka 7. Katswili wina wa Baibulo anacha ulali-kiwu kuti “nkhani yothandiza,” ndipo anakambakuti colinga ca ulalikiwo ndi “kutitsogolela pau-

Buku Losavuta Kumvetsetsa

Kuti mudziwe zambili pa-nkhani ya mmene moyounayambila, onani kabukukakuti Was Life Created?kofalitsidwa ndi Mboni zaYehova. Kabukuka kapeze-kanso pa www.jw.org.

˘DigitalV

isionLtd/

agefotostoc

k

Kodi Baibulo

L I L I N D I U T H E N G A W O T A N I ?

Na. 1 2016 5

˙ Baibulo lili ndi mabuku opatulika okwana 66.

˙ Mabuku ena a m’Baibulo amafotokoza zambili yakale, malamulo, ulosi, ndakatulo,miyambo, nyimbo, ndi makalata.

˙ Linayamba kulembedwa mu 1513 B.C.E., ndipolinatha mu 98 C.E. Linalembedwa kwa zakazoposa 1,600.

˙ Amuna 40 analemba Baibulomouzilidwa ndi Mulungu.

Dziwani Izi Ponena za Baibulo

Kuti mudziwe zambilizokhudza Baibulo, ona-ni kabuku kakuti KodiBaibulo Lili Ndi Uthe-nga Wotani?kofalitsidwa ndi Mboniza Yehova. Kabukukakapezekanso pawww.jw.org.

moyo wathu, osati kutidziwitsa zinthu zosiyanasi-yana. Mungawelenge macaputala amenewo mwinakwa mphindi 15 kapena 20, ndipo mudzadabwa ndimau a Yesu osavuta koma amphamvu kwambili.Mbali yaciwili imene imacititsa Baibulo kukha-

la losavuta kumvetsetsa ndi nkhani zake. Baibu-lo si buku la nthano. Buku lakuti The World BookEncyclopedia linakamba kuti Baibulo ndi buku li-mene “limakamba za anthu apamwamba ndi otsi-ka,” komanso “zolinga zao, zolakwa zao, ndi zipa-mbano zao.” Si covuta kumvetsetsa ndi kufotokozankhani za anthu enieni amenewo, ndiponso zimenetimaphunzila kwa io.—Aroma 15:4.

LIKUPEZEKA M’ZINENELO ZAMBILIKuti mumvetsetse zimene mukuwelenga m’buku,

ilo liyenela kukhala la cinenelo cimene mudziwa.Mwacionekele, Baibulo nalonso likupezeka m’cine-nelo cimene mumamvetsetsa, mosasamala kanthuza kumene mumakhala kapena mtundu wanu. Ona-ni nchito imene imakhalapo kuti Baibulo lizipezekam’zinenelo zambili.Nchito Yomasulila. Poyamba, Baibulo linale-

mbedwa m’Ciheberi, m’Ciaramu, ndi m’Cigiriki.Izi zinacititsa kuti liziwelengedwa ndi anthu oce-pa. Pofuna kuti Baibulo lipezeke m’zinenelo zina-nso, omasulila mabuku akhala akugwila nchitomwa-khama. Cifukwa ca khama lao, Baibulo likupezeka

m’zinenelo pafupifupi 2,700 kaya lathunthu kapenambali yake. Izi zitanthauza kuti anthu oposa 90 paanthu 100 alionse ali ndi Baibulo m’cinenelo cao.Nchito Yofalitsa Mabuku. Poyamba, Baibulo li-

nalembedwa pazinthu zosacedwa kuonongeka, mo-nga pamipukutu yamapepala a gumbwa ndi zikopa.Kuti uthengawo ufalikile, anali kukopela zolembe-dwazo bwinobwino ndi manja. Makope amenewoanali okwela mtengo, ndipo ndi anthu ocepa ame-ne anali kupezeka nao. Komabe, pogwilitsila nchi-to makina osindikizila amene Gutenberg anapa-nga zaka zoposa 550 zapitazo, Baibulo linayambakufalitsidwa kwambili. Mabaibulo oposa 5 biliyoniafalitsidwa, kaya athunthu kapena mbali yake.Palibe buku lina lacipembedzo limene limafa-

nana ndi Baibulo pa mfundo zimene tafotokoza-zi. Kukamba zoona, Baibulo ndi buku losavuta ku-mvetsa. Komabe, ena zimawavuta kulimvetsetsa.Ngakhale n’conco, thandizo lilipo. Kodi mungalipe-ze kuti? Nanga mungapindule bwanji?

ˆWelengani

nkhani yotsatila kuti mudziwe mayankho a mafunsoamenewa.

Baibulo limapeleka mayankhoogwila mtima a mafunsoofunika kwambili

6 NSANJA YA MLONDA

Yelekezani kuti mwapita kukaceza kudziko lacilendokwa nthawi yoyamba. Ndiyeno, kumeneko mwape-za anthu, zikhalidwe, zakudya, ndi ndalama zimeneinu simunazionepo. Mosakaikila, mungakhumudwekwambili.Mungamve cimodzimodzi pamene muwelenga Bai-

bulo kwa nthawi yoyamba. Mukamaliwelenga, lima-kubwezani kumbuyo kudziko lakale limene lingaone-ke ngati lacilendo kwa inu. Kudzikolo, mwapezakoanthu ochedwa Afilisiti, zikhalidwe zacilendo mo-nga ‘kung’amba zovala,’ cakudya cochedwa mana,ndi ndalama yodziwika kuti dalakima. (Ekisodo 16:31;Yoswa 13:2; 2 Samueli 3:31; Luka 15:9) Zinthu zi-menezi zingakhale zosamvetsetseka kwa inu. Mofa-nana ndi mmene zingakhalile mukapita kudziko laci-lendo, mosakaikila inunso mungayamikile kwambilimunthu wina atafotokozelani zinthu zina ndi zina zam’Baibulo.

THANDIZO LIMENE LINALIPO M’NTHAWI YAKALEKucokela mu 1500 B.C.E., pamene malemba opatu-

lika anayamba kulembedwa, thandizo lakhala liku-pelekedwa n’colinga cakuti anthu amvetsetse male-mba. Mwacitsanzo, Mose, mtsogoleli woyamba wamtundu wa Isiraeli, “anayamba kufotokoza” zinthuzolembedwa.—Deuteronomo 1:5.Zaka 1,000 zapitazo, aphunzitsi odziwa bwino Ma-

lemba analipo. Mu 455 B.C E., gulu la Ayuda, ku-phatikizapo ana ambili, anasonkhana m’bwalo laliku-lu mu mzinda wa Yelusalemu. Aphunzitsi a Baibuloanali “kuwelenga bukulo [lopatulika] mokweza.”Koma anacitanso zambili. “Iwo anapitiliza kutha-ndiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene analikuwelenga.”—Nehemiya 8:1-8.Pambuyo pa zaka 500, Yesu Kristu nayenso ana-

li kugwila nchito yophunzitsa imeneyi. Anthu analikumudziwa kuti ndi mphunzitsi. (Yohane 13:13) Iyeanali kuphunzitsa gulu la anthu komanso munthualiyense payekha. Pa nthawi ina, anaphunzitsa kha-mu la anthu pa Ulaliki wake wochuka wa pa Phili,

ndipo “khamu la anthulo linakhudzidwa moti linada-bwa ndi kaphunzitsidwe kake.” (Mateyu 5:1, 2; 7:28)M’caka ca 33 C.E.,Yesu anakamba ndi ophunzila akeawili pamene anali kuyenda pa njila yopita kumudziwina pafupi ndi Yelusalemu, ndipo ‘anawafotokozelaMalemba momveka bwino.’—Luka 24:13-15, 27, 32.Ophunzila a Yesu analinso alangizi a Mau a Mulu-

ngu. Pa cocitika cina, nduna ya ku Itiyopiya inali ku-welenga mbali ina ya m’Malemba. Wophunzila Filipoanafikila ndunayo ndi kuifunsa kuti: “Kodi mukumve-tsa zimene mukuwelengazo?” Poyankha ndunayo ina-ti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulila?”Pamenepo Filipo anayamba kumufokokozela tantha-uzo la zimene anali kuwelenga.—Machitidwe 8:27-35.

THANDIZO LIMENE LILIPO MASIKU ANOMofanana ndi aphunzitsi a Baibulo a m’nthawi ya-

kale, Mboni za Yehova masiku ano zikugwila nchi-to yophunzitsa anthu m’maiko 239 padziko lonse.(Mateyu 28:19, 20) Mlungu uliwonse, Mboni zaYeho-va zimathandiza anthu oposa 9 miliyoni kumvetse-tsa Baibulo. Ambili mwa anthuwa sadziwa zambiliza Cikristu. Kuphunzila Baibulo ndi kwaulele ndi-po mungaphunzilile panyumba panu kapena pamaloaliwonse amene mufuna. Ena amaphunzila Baibulopa foni, pakompyuta kapena pa cipangizo ciliconsecokhala ndi intaneti.Ngati mufuna kudziwa zambili za mmene mungapi-

ndulile ndi makonzedwe amenewa, funsani wa Mboniza Yehova aliyense. Mudzaona kuti Baibulo si bukulovuta kumvetsetsa, koma ‘ndi lopindulitsa pa kuphu-nzitsa, kudzudzula, kuongola zinthu ndi kulangizam’cilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woye-nelela bwino ndi wokonzeka mokwanila kucita nchitoiliyonse yabwino.’—2 Timoteyo 3:16, 17. ˇ

Pemphani Thandizo KutiMumvetsetse Baibulo

Mungacite daunilodi Baibulo kapenakupempha phunzilo la Baibulo pa

intaneti pogwilitsila nchito webusaitiyathu ya www.jw.org

Onelelani vidiyo yaku-ti, N’cifukwa CianiMuyenela KuphunzilaBaibulo?pa www.jw.org

wOnelelani vidiyo yakutiKodi Phunzilo la BaibuloLimacitika Bwanji?pa www.jw.org

w

Mafunso ofunsidwa kawilikawiliˇ Kodi colinga ca moyo n’ciani?ˇ N’cifukwa ciani anthu amafa?ˇ Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila?

(Pitani polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ˛

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO)

Nkhani zaumwiniˇ Zimene mungacite ngati muli ndi nkhawaˇ Kupilila matenda aakuluˇ Mavuto azacuma ndiponso ngongole

(Pitani polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ˛

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO)

Zothandiza mabanjaˇ Zimene mungacite kuti musamakanganeˇ Mmene mungalele bwino anaˇ Kuphunzitsa ana mfundo za makhalidwe abwino

(Pitani polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ˛

ANTHU APABANJA NDIPONSO MAKOLO)

Malangizo kwa acinyamataˇ Mmene mungacitile ndi nkhanza za kugonanaˇ Zimene mungacite ngati anthu ena akukuvutitsaniˇ Zimene mungacite ngati mulibe mnzanu

(Pitani polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ˛

ACINYAMATA)

Thandizo la paWebusaiti

Kodi mungakonde kuphunzila Baibulopanokha? Pitani pa webusaiti ya jw.org kutimuyambe kuphunzila. Webusaiti imeneyiidzakuthandizani kudziwa zambili zokhudzaBaibulo kwaulele m’zinenelo zoposa 700.Mudzakondwela kudziwa nkhani zotsatilazi:

s

8 NSANJA YA MLONDA

PANAYIOTA anakulila pacilumba cina ca kuMediterranean. Ali wacitsikana, anali kukonda

kwambili zandale. Patapita nthawi, anakhala ka-lembela wa cipani candale cimene cinali m’mudziwao. Iye analinso kupita kunyumba ndi nyumba ku-pemphetsa ndalama za cipani cao. Koma m’kupi-ta kwa nthawi, Panayiota anakhumudwa kwambili.Ngakhale kuti mamembala a cipani cao anali kugwi-lizana kwambili, makhalidwe monga kukondela, ku-funa kuchuka, mikangano, ndi nsanje zinali zofala.Daniel analeledwa m’banja lokonda za cipembe-

dzo ku Ireland. Ngakhale n’telo, iye akumbukilabwino cinyengo ca abusa amene anali kuledzela, ku-chova njuga, ndi kuba ndalama za m’mbale ya zope-leka kwinaku akumuphunzitsa kuti ngati wacimwaadzaochedwa ku moto wa helo.Jeffery wakhala akucita zamalonda ndi maka-

mpani a masitima apamadzi ocokela m’maiko aUnited Kingdom ndi United States. Iye akumbukilazocitika zosiyanasiyana pamene makasitomala ndiocita zamalonda anali kucita zinthu mwacinyengopokambilana ndi akuluakulu a boma. Anali kucitazimenezi n’colinga cakuti asunge mapangano ao.Izi ndi zitsanzo zocepa cabe za anthu amene ama-

cita cinyengo. Masiku ano, cinyengo cili paliponsekaya m’zandale, m’zacipembedzo kapena m’zama-londa. Liu lacingelezi lomasulidwa kuti “cinyengo”

linacokela ku liu la cigiriki limene limakamba za oci-ta masewelo amene kawilikawili amadzibisa nkhopekuti anthu asawadziwe. M’kupita kwa nthawi, anthuanayamba kusewenzetsa liu limeneli pofuna kuka-mba za munthu amene amacita zinthu mwacinye-ngo kuti apeze zimene afuna.Cinyengo cingapangitse anthu ena kukhumudwa

ndi kukwiya kwambili. Mokhudzidwa mtima, ioangafunse kuti: “Kodi Cinyengo cidzatha?” Mau aMulungu amatitsimikizila kuti cinyengo cidzatha.

MMENE MULUNGU NDI MWANAWAKE AMAONELA CINYENGOBaibulo limafotokoza mmene cinyengo cinaya-

mbila. Limatiuza kuti cinyengo cinayambila ku-mwamba ndi colengedwa cauzimu osati anthu. Pa-ciyambi, Satana mdyelekezi kupitila mwa njokamonga cobisalilamo, ananamiza Hava, mkazi wo-yamba ndipo anadzionetsa ngati wabwino pofu-na kum’soceletsa. (Genesis 3:1-5) Kucokela nthawi-yo, anthu ambili amacita zinthu mwacinyengo kutiakwanilitse zolinga zao zadyela.Mtundu wa Aisiraeli utayamba kulambila kona-

ma ndiponso kucita cinyengo ca kuuzimu, Mulu-ngu anawacenjeza mobwelezabweleza za zotsati-lapo zake. Kupitila mwa mneneli Yesaya, YehovaMulungu anati: “Anthu awa ayandikila kwa ine ndi

CINYENGO Kodi Cidzatha?

Na. 1 2016 9

pakamwa pao pokha, ndipo andilemekeza ndi milo-mo yao yokha koma mtima wao auika kutali ndiine.” (Yesaya 29:13) Mtunduwo utalephela kusi-ntha, Mulungu analola olamulila amphamvu kuti ao-nonge Yerusalemu ndi kacisi wake, likulu la cipe-mbedzo ca Aisiraeli. Coyamba, Ababulo anaonongaYerusalemumu 607 B.C.E., kenako asilikali a Aromaanaononga mzindawo mu 70 C.E. Kukamba zoona,Mulungu salekelela zacinyengo.Mulungu ndi Mwana Wake, Yesu, amakonda

anthu amene ndi oona mtima ndi opanda cinye-ngo. Mwacitsanzo, kuciyambi kwa utumiki waYesu, mwamuna wina dzina lake Natanayeli ana-bwela kwa iye. Atamuona, Yesu anati: “Onani Mwi-siraeli ndithu, amene mwa iye mulibe cinyengo.”(Yohane 1:47) Natanayeli amene anali kuchedwansokuti Batolomeyo, anakhala mmodzi wa atumwi 12 aYesu.—Luka 6:13-16.Nthawi zambili Yesu anali kukhala ndi ophunzi-

la ake, ndipo anali kuwaphunzitsa zinthu zokhu-dza Mulungu. Iwo sanafunike kukhala acinyengo.Pofuna kuwacenjeza, Yesu anatsutsa mwamphamvuatsogoleli acipembedzo a m’nthawiyo amene analiacinyengo. Onani mmene io anali kucitila zimenezi.Anali kucita “cilungamo” kuti anthu awaone. Yesu

anauza omvela ake kuti: “Samalani kuti musama-cite cilungamo canu pamaso pa anthu ndi coli-nga cakuti akuoneni . . . muja amacitila onyenga.”Iye anawauzanso kuti azipeleka mphatso zacifundo‘mwamseli’ kapena kuti mosaonetsela. Iwo anafuni-kanso kupemphela mwamseli osati modzionetselakwa anthu. Kucita zimenezo kukanapangitsa kula-mbila kwao kukhala kovomelezeka kwa Atate wake.—Mateyu 6:1-6.Anali kuweluza ena mwamsanga. Yesu anati: “Wo-

nyenga iwe! Yamba wacotsa mtanda wa denga lanyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatelo udzathakuona bwino mmene ungacotsele kacitsotso m’disola m’bale wako.” (Mateyu 7:5) Ngati munthu amaga-nizila kwambili zolakwa za ena m’malo moganizilazolakwa zake zazikulu, amadzipanga kukhala mu-nthu wosiyana ndi mmene alili. Zoona zake n’zakutianthu “onse ndi ocimwa ndipo ndi opelewela paulemelelo wa Mulungu.”—Aroma 3:23.Anali kubisa zolinga zao zoipa. Panthawi ina,

ophunzila a Afarisi ndi acipani ca Herode anafi-

ka kwa Yesu ndi kumufunsa pankhani yamsonkho. Pofuna kumukopa, io anati: “Mphu-nzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndi-po mumaphunzitsa njila ya Mulungu m’coona-di.” Kenako pofuna kumuyesa anamufunsa kuti:“Kodi n’kololeka kupeleka msonkho kwa Kaisa-ra kapena ai?” Yesu anawayankha kuti: “Onyengainu! Bwanji mukundiyesa?” Moyenelela Yesu anawa-cha kuti onyenga cifukwa sanali kufuna kumva ya-nkho la funso lao, koma anali kufuna kuti “am’kolem’mawu ake.”—Mateyu 22:15-22.Pamene mpingo wacikristu unakhazikitsidwa

pa Pentekosite mu 33 C.E., coonadi ndi kuonamtima zinayamba kuonjezeka. Akristu oona ana-cita khama kuthetsa cinyengo ciliconse cime-ne anali naco. Mwacitsanzo, Petulo mmodzi waatumwi 12, analimbikitsa Akristu anzake kuti akha-le ‘omvela coonadi ndi kukonda abale mopanda

cinyengo.’ (1 Petulo 1:22) Mtumwi Paulo, anali-mbikitsa anchito anzake kuti akhale ndi “ciko-ndi cocokela mumtima woyela, m’cikumbumti-ma cabwino, ndiponso m’cikhulupililo copandacinyengo.”—1 Timoteyo 1:5.

MPHAMVU YA MAU A MULUNGUZimene Yesu ndi atumwi ake anali kuphunzitsa,

n’zothandiza kwambili masiku ano monga mme-ne zinalili m’nthawi ya atumwi. Pankhani imeneyi,mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu aMulungu ndiamoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kupo-sa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amala-sa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndimzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta am’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikilazimene munthu akuganiza komanso zolinga za mti-ma wake.” (Aheberi 4:12) Kudziwa zimene Baibulo

Akristu oona amaonetsana “cikondicocokela mumtima woyela,m’cikumbumtima cabwino, ndiponsom’cikhulupililo copanda cinyengo.”—1 TIMOTEYO 1:5

10 NSANJA YA MLONDA

limaphunzitsa ndi kuyesetsa kucita zimene limaka-mba, kwathandiza anthu ambili kusiya cinyengo ndikuyamba kucita cilungamo. Kumbukilani zitsanzozitatu za anthu amene tawachula poyamba aja.Panayiota anasintha umoyowake, pamene anape-

zeka pamisonkhano ya mpingo ku Nyumba ya Ufu-mu ya Mboni za Yehova. Kumeneko, iye sanaonemunthu aliyense akucita zinthu mwacinyengo pofu-na kukondweletsa ena. Panayiota anati: “Pamiso-nkhano imeneyi, ndinaona anthu akuonetsana ci-kondi ceniceni, cimene sindinacionepo zaka zonsezimene ndinali kucita zandale.”Panayiota anayamba kuphunzila Baibulo kena-

ko anabatizidwa. Iye wakhala m’coonadi zaka 30tsopano. Iye anati: “Tsopano ndili ndi moyo waphi-ndu, osati cifukwa copita kunyumba ndi nyumba

kupemphetsa ndalama za cipani, koma cifukwa co-lalikila za Ufumu wa Mulungu, umene udzabweletsacilungamo padziko lapansi.”Daniel anapita patsogolo mwakuuzimu ndipo

anapatsidwa maudindo osiyanasiyana. Patapitazaka zocepa, iye analakwitsa zinazake ndipo ciku-mbumtima cake cinayamba kumuvutitsa. Iye anati:“Nditakumbukila za cinyengo cimene cinali m’chali-chi canga cakale, ndinasankha kutula pansi maudi-ndo amenewa. Sindinali kufuna kuti Akristu anza-nga aziona kuti ndine munthu wabwino pamenesindinali conco.”Patapita nthawi, Daniel anasintha ndipo anaya-

mbanso kutumikila pa maudindo ake mumpingo alindi cikumbumtima cabwino. Kuona mtima kotelekumapezeka kokha pakati pa anthu amene amatu-mikila Mulungu mopanda cinyengo. Iwo aphunzilakucotsa “mtandawa denga” m’masomwao asanaco-tse “kacitsotso” m’maso mwa m’bale wao.Jeffery amene anali kucita zamalonda, anati:

“Nditapita patsogolo kuphunzila Baibulo, ndina-zindikila kuti sindiyenela kucita cinyengo pocitapangano la zamalonda. Ndinakhala ndi cikumbu-mtima cabwino cifukwa cowelenga Malemba mo-nga Miyambo 11:1 limene limakamba kuti ‘masike-lo acinyengo amam’nyansa Yehova.’” Mosiyana ndianthu amene anafunsa Yesu funso lokhudza mso-nkho, Jeffery anaphunzila kuthetsa maganizo ola-kwika pocita zinthu ndi Akristu anzake ndi anthuena.Mboni za Yehova mamiliyoni padziko lonse zima-

yesetsa kucita zimene zaphunzila m’Baibulo. Izozimayesetsa “kuvala umunthu watsopano umeneunalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungundipo umatsatila zofunika pa cilungamo cenicenindi pa kukhulupilika.” (Aefeso 4:24) Tikupemphanikuti mudziwe zambili zokhudza Mboni za Yehova,zimene zimakhulupilila, ndi mmene zingakuthandi-zileni kudziwa zimene Mulungu walonjeza kudzaci-ta m’dziko latsopano. M’dziko limenelo “mudzakha-la cilungamo” ndipo cinyengo sicidzakhalamonso.—2 Petulo 3:13. ˇ

“Ndinaona anthuakuonetsana cikondiceniceni.”—PANAYIOTA

“Sindinali kufuna kutiAkristu anzanga azionakuti ndine munthuwabwino pamenesindinali conco.”—DANIEL

“Ndinazindikila kutisindiyenela kucitacinyengo. . . .Ndinakhala ndicikumbumtimacabwino.”—JEFFER

Lemba la Machitidwe 2:5-11 lionetsa kuculuka kwa anthu amene ana-pezeka pa Pentekosite mu 33 C.E.Wolemba nkhani wina waciyuda, dzi-na lake Philo, anatsimikizila zimenezi.

Ponena za anthu amene anali kupita ku Yerusalemu, Philo anale-mba kuti: “Anthu osawelengeka, ocokela m’mizinda yosawelengeka,ena ocokela kum’mawa, kumadzulo, kum’mwela, ndi kumpoto, anali ku-bwela kucikondwelelo ciliconse. Ndipo ena anali kuyenda wa pansi, ka-pena pa bwato.” Iye anagwilansomau amu kalata ya AgiripaWoyamba,mdzukulu wa HerodeWamkulu, yopita kwa MfumuYaciroma dzina lakeKaligula. M’kalatayi, Agiripa analemba zokhuza Yerusalemu kuti: “Mzi-nda Woyela . . . si mzinda wa dziko la Yudeya cabe ai, koma ndi wa ma-iko ena ambili kuphatikizapo oyandikana nalo. Izi zili conco cifukwa ca-kuti maiko enawa akhala akulamulidwa ndi mafumu aciyuda.”

Mfumu Agripa analemba maiko amene mafumu aciyuda analikulamulila kuphatikizapo madela akutali monga Mesopotamiya, ku-mpoto kwa Africa, Asia Minor, Girisi, ndi zilumba za pa nyanja yaMediterranean. Katswili wina wa zamaphunzilo, dzina lake JoachimJeremias, analemba kuti: “Ngakhale kuti zimene Agripa analembasizichula mwacindunji za maulendo opita ku Yerusalemu, mfundo ndiyakuti anthu anali kupita ku Yerusalemu cifukwa Ayuda onse aciku-lile anali kulamulidwa kupanga maulendo amenewa.—Deuteronomo16:16 ˇ

KODI MUDZIˆWA?

Kodi Ayuda amene anapezeka pa Pentekosite mu33 C.E. anacokeladi “mu mtundu uliwonse mwamitundu ya pansi pa thambo”?

NJILA ZODZAZIDWA NDI ANTHU KUYERUSALEMU PA PENTEKOSITE

MU 33 C.E

Ayuda anali kucita zikondwelelo zitatu caka ciliconse kuYerusalemu. Zi-kondwelelo zimenezi ndi Pasika, Pentekosite, ndi Cikondwelelo ca Misa-sa. M’nthawi ya Atumwi, anthu masauzande ambili anali kupita kuYeru-salemu kukacita zikondwelelo zimenezi. Anthu amenewa anali kucokelam’dziko la Aisiraeli ndiponso m’dziko lililonse kumene kunali kukha-la Ayuda. (Luka 2:41, 42; Machitidwe 2:1, 5-11) Conco, alendo onseamene anali kufika pa zikondwelelo zimenezi anali kufunika kupezamalo ogona.

Ena anali kugona m’nyumba za anzao, ndipo ena anali kugona kunyumba za alendo. Ambili anali kumanga misasa yogonamo mkati ka-pena kunja kwa mzinda. Pa tsiku lothela kukhala ku Yerusalemu, Yesuanakagona mumzinda wapafupi wa Betaniya. (Mateyu 21:17)

Mabwinja a nyumba zingapo amene anali pafupi ndi pamene pana-li kacisi apezeka ndi mabeseni osambilamo. Anthu amaganiza kutim’nyumba zimenezi ndi mmene anthu anali kugona ndiponso kudziye-letsa asanalowe m’kacisi. Mau amene analembedwa pa cipupa ca nyu-mba ina, akuonetsa kuti munthu wina dzina lake Theodotus, ameneanali wansembe ndiponso mtsogoleli wa sunagoge, ndi amene “ana-manga sunagoge wowelengelamo Tora . . . komanso nyumba yogonaanthu ambili, zipinda, ndiponso mabeseni osungilamo madzi.” ˇ

Kodi anthu masauzande ambili amene anali kubwelakuYerusalemu kudzacita zikondwelelo zaciyudaanali kugona kuti?

DZIWE LAKALE LOSAMBILAMOKU YERUSALEMUTodd Bolen/BiblePlaces.com

Na. 1 2016 11

TSOPANO ndi nthawi yakuti Timoteyo acoke pa-nyumba ndi kusiya makolo ake. Maganizo ake

onse ali pa utumiki umene akuyembekezela kucita.Anzake ndi amene akutsogolela podutsa m’madelaamene Timoteyo akudziwa bwino. Atayenda kamtu-nda ndithu, mzinda wa Lusitara umene uli pamwa-mba pa phili, uyamba kubisika. Timoteyo akumwe-tulila pamene akuganizila amai ake ndi agogo ake,amene akumunyadila uku akupukuta misozi pameneiye akucoka. Kodi angabwelele ndi kukawatsanzikakomaliza?Mtumwi Paulo akayang’ana Timoteyo anali ku-

mwetulila. Iye anali kudziwa kuti Timoteyo anali ndimanyazi ofunika kuwathetsa. Ngakhale n’conco, Pa-ulo anakondwela kuona kuti mnyamatayo anali wo-dzipeleka. Timoteyo anali wacipepele, mwina wazaka za m’ma 20, ndipo anali kulemekeza ndi kuko-nda kwambili Paulo. Timoteyo anapitila limodzi ndiPaulo, mwamuna wokhulupilika ndi wamphamvu pa-ulendo wautali kwambili. Iwo anali kuyenda wapa-nsi kapena kukwela bwato, ndipo m’njila anali kuku-mana ndi zoopsa zosiyanasiyana. Timoteyo sanalikudziwa ngati adzabwelelanso kunyumba.N’cifukwa ciani mnyamatayu anasankha utumiki

umenewu? Ndi madalitso otani amene munthu anga-peze cifukwa codzipeleka? Nanga cikhulupililo caTimoteyo cingatilimbikitse bwanji?

“KUYAMBILA PAMENE UNALI WAKHANDA”Tiyeni tibwelele kumbuyo zaka ziwili kapena zitatu

mumzinda wa Lusitara, kumene Timoteyo anali ku-khala. Lusitara unali mzinda waung’ono umene unalikudela la kumidzi m’cigwa cokhala ndi madzi ambili.Anthu akumeneko ayenela kuti anali kumva cinenelo

ca Cigiriki, koma anali kukamba Cilukaoniya cimenecinali cinenelo cao. Tsiku lina mumzinda wa Lusita-ra umenewo munabuka cipolowe. Amishonale awiliAcikristu, mtumwi Paulo ndi Baranaba, anafika mu-mzindawo kucokela ku Ikoniyomzindawaukulu ume-ne unali pafupi. Pamene io anali kulalikila poyela,Paulo anaona mwamuna wina wolemala amene analindi cikhulupililo colimba. Conco, Paulo anacilitsamwamunayo mozizwitsa.—Machitidwe 14:5-10.Zioneka kuti kale anthu ambili a ku Lusitara ana-

li kukhulupilila kuti milungu yao imadzisandu-tsa anthu. Motelo, anacha Paulo kuti Heme ndipoBaranaba anamucha kuti Zeu. Akristu awili odzice-petsa amenewa, anavutika kuletsa khamu la anthulokupeleka nsembe kwa io.—Machitidwe 14:11-18.Ngakhale zinali conco, anthu ocepa a ku Lusi-

tara anadziwa kuti Paulo ndi Baranaba sanali mi-lungu yao yonama, koma anali anthu enieni ame-ne anawabweletsela uthenga wabwino. Mwacitsanzo,Yunike mkazi waciyuda amene anakwatiwa ndi mwa-muna wacigiriki wosakhulupilila,� pamodzi ndi amaiake a Loisi, anamvetsela mosamalitsa kwa Paulo ndiBaranaba. Iwo anali kulalikila za uthenga wabwinoumene m’Yuda aliyense wokhulupilika anali kufunakuumva. Uthengawo unali kunena za kubwela kwaMesiya ndi kukwanilitsidwa kwa maulosi okamba zaiye olembedwa m’Malemba.Ganizilani mmene Timoteyo anamvelela pame-

ne Paulo anabwela mumzindawo. ‘Kuyambila pa-mene anali wakhanda,’ Timoteyo anaphunzitsi-dwa kukonda Malemba oyela Aciheberi. (2 Timoteyo3:15) Mofanana ndi amai ake ndi agogo ake, iye

� Onani mutu wakuti “Kodi Mudziwa?” m’magazini ino.

TSANZILANI CIKHULUPILILO CAO � TIMOTEYO

“MwanaWangaWokondedwa ndiWokhulupilika mwaAmbuye”

12 NSANJA YA MLONDA

anaona kuti Paulo ndi Baranaba anali kukamba zoo-na zokhudza Mesiya. Iye anaganizilanso za mwamu-na wolemala amene Paulo anacilitsa. Kungocokelaali mwana, Timoteyo anali kuona mwamuna wole-mala ameneyu nthawi zambili m’miseu ya ku Lusi-tara. Timoteyo anaona mwamunayo akuyenda kwanthawi yoyamba. Cifukwa ca zimenezi, Yunike ndiLoisi pamodzi ndi Timoteyo anakhala Akristu. Masi-ku ano, makolo angaphunzilepo zambili pa citsanzoca Loisi ndi Yunike. Kodi inu ndinu citsanzo cabwinokwa acicepele?

“TIYENELA KUKUMANA NDI MASAUTSO AMBILI”Anthu amene anakhala Akristu ku Lusitara, ayene-

la kuti anakondwela kwambili atadziwa za ciyembe-kezo cimene otsatila a Kristu anali naco. Anadzi-wanso kuti kukhala wophunzila kunali ndi mavutoake. Mwacitsanzo, Ayuda otsutsa ocokela ku Ikoniyondi ku Antiokeya anafika ndi kusonkhezela anthu amumzindawo kuti aukile Paulo ndi Baranaba. Posa-khalitsa, khamu la anthu aciwawa linafika ndi ku-yamba kuponya Paulomiyala. Iwo anamponyamiyalamobwelezabweleza cakuti iye anagwa pansi. Ndi-yeno, anthuwo anamukokela kunja kwa mzindawopoganiza kuti wafa.—Machitidwe 14:19.Koma ophunzila a ku Lusitara anapita kwa Paulo

ndi kumuzungulila. Iwo anakondwela kwambili atao-na kuti Paulo wadzuka, ndi kuti walimba mtima kupi-

tanso mumzinda umenewo. Tsiku lotsatila, iye ndiBaranaba anacoka ndi kupita ku Debe kukalalikila.Atapanga ophunzila atsopano kumeneko, io moli-mba mtima anabwelelanso ku Lusitara ngakhale kutikucita zimenezo kunali koopsa kwambili. N’cifukwaciani anabwelela? Nkhaniyo imatiuza kuti kumeneko“anali kulimbitsa mitima ya ophunzila ndi kuwalimbi-kitsa kuti akhalebe m’cikhulupililo.” Ganizilani kutimukuona Timoteyo akumvetsela mwachelu pamenePaulo ndi Baranaba akuuza Akristu amenewo kuti,ciyembekezo cao camtsogolo n’camtengo wapatalikuposa zimene akukumana nazo. Iwo anati: “Tiyene-la kukumana ndi masautso ambili kuti tikalowe muufumu wa Mulungu.”—Machitidwe 14:20-22.Timoteyo anaona kuti Paulo anali kutsatila mau

amenewa paumoyo wake. Ndipo sanali kucita ma-ntha kukumana ndi masautso, n’colinga cakuti ala-likila uthenga wabwino kwa ena. Conco, Timoteyoanadziwa kuti akatengela citsanzo ca Paulo, anthu aku Lusitara kuphatikizapo atate ake adzamutsutsa.Koma iye sanalole kuti nkhawa imeneyi imulephele-tse kusankha kutumikila Mulungu. Masiku ano, paliacicepele ambili amene ali ngati Timoteyo. Iwomwa-nzelu amasankha anthu amene ali ndi cikhulupililocolimba kuti akhale anzao, kuti aziwathandiza ndikuwalimbikitsa. Ndiponso salola citsutso kuwacititsakuleka kutumikila Mulungu woona.

Timoteyo anamvetsela mwachelu pamene mtumwi Paulo anali kuphunzitsa

“ABALE . . . ANAMUCITILA UMBONI WABWINO”Monga mmene takambila poyamba paja, Paulo

ayenela kuti anacezelanso mzinda wa Lusitara pata-pita zaka ziwili kapena zitatu. Ganizilani cimwemwecimeneTimoteyo,Yunike, ndi Loisi anali naco poonakuti Paulo wabwelansomumzindawo, koma panthawiino ali pamodzi ndi Sila. Mosakaikila, Paulo nayensoanakondwela kwambili. Iye anaona zotsatilapo za-bwino cifukwa ca mbeu za coonadi zimene anabzalaku Lusitara. Loisi ndi mwana wake Yunike, anali ata-khala akazi okhulupilika Acikristu, odzala ndi “ci-khulupililo copanda cinyengo,” cimene Paulo ana-yamikila kwambili. (2 Timoteyo 1:5) Nanga bwanjiponena za wacicepele Timoteyo?Paulo anapeza kuti mnyamatayu wapita patsogolo

kwambili kucokela paulendo wake wapita. Abale a kuLusitara ndi ku Ikoniyo, mzinda umene uli pa mtu-nda wa makilomita 32 kucoka ku Lusitara, ‘anamuci-tila umboni wabwino’ Timoteyo. (Machitidwe 16:2)N’ciani cinam’thandiza kukhala ndi mbili yabwinoimeneyi?“Malemba oyela” amene Timoteyo anaphunzitsi-

dwa ndi amai ake ndiponso agogo ake ‘kuyambilapamene anali wakhanda,’ anaphatikizapo malangizoothandiza kwa acinyamata. (2 Timoteyo 3:15) Mwa-citsanzo, Baibulo limati: “Kumbukila Mlengi wakoWamkulu masiku a unyamata wako.” (Mlaliki 12:1)Mau amenewa anam’thandiza kwambili Timoteyoatakhala Mkristu. Iye anazindikila kuti njila yabwinokoposa imene angakumbukile Mlengi wakeWamkulundi kulalikila uthenga wabwino wokamba za Kristu,Mwana wa Mulungu. M’kupita kwa nthawi, Timoteyoanaphunzila kuthetsa manyazi amene anali kumule-pheletsa kuuza ena uthenga wabwino wokamba zaYesu Kristu.Abale amene anali kutsogolela m’mipingo anao-

na kuti Timoteyo akupita patsogolo. Mosakaikila, ioanacita cidwi kuona mmene mnyamatayu anali ku-pitila patsogolo, ndiponso mmene analili citsanzocabwino kwa ena. Koposa zonse, Yehova anali ku-ona citsanzo cabwino ca Timoteyo. Mulungu ana-uzila maulosi ena okhudza Timoteyo, mwina analiokamba za utumiki umene anali kudzacita potha-ndiza mipingo yambili. Pamene Paulo anawacezela-nso, anaona kuti Timoteyo angawathandize kwambi-li pamaulendo ake aumishonale. Abale a ku Lusitara

anavomeleza zimenezo. Abalewo anaika manja ao pamnyamatayu, kuonetsa kuti wapatsidwa udindo wa-padela mu utumiki waYehovaMulungu.—1 Timoteyo1:18; 4:14.Timoteyo anasowa cokamba cifukwa ca udindo

waukulu umene anapatsidwa. Iye anali wokonzekakupita.� Koma kodi atate ake osakhulupilila anamve-la bwanji pamene mwana wao anasankha kukhalamtumiki woyendayenda wacikristu? Mwacionekele,io anali kufuna kuti mwana wao akhale ndi tsogololosiyana kwambili ndi zimene mwanayo anasankha.Nanga bwanji amai ake ndi agogo ake? Iwo anamu-nyadila kwambili Timoteyo. Koma panthawi imodzi-modzi anali kumudela nkhawa, ndipo n’zacibadwamakolo kumva conco.Koma zoona zake n’zakuti Timoteyo anasankha

kupita. Iye anayamba kuyenda ndi mtumwi Pau-lo. Anasiya zinthu zonse zimene anali nazo mumzi-nda wa Lusitara. Atayenda ulendo wa tsiku limodzi,amuna atatu amenewa anafika mumzinda wa Ikoni-yo. Ndiyeno, Timoteyo anayamba kuphunzila mme-ne Paulo ndi Sila anali kupelekela malangizo atso-pano ocokela ku bungwe lolamulila ku Yerusalemu,ndiponso mmene anali kulimbitsila cikhulupililo caophunzila ku Ikoniyo. (Machitidwe 16:4, 5) Ici cinaliciyambi cabe.Atacezela mipingo ya ku Galatiya, amishonale

amenewo anacoka. Iwo anayenda makilomita ambilikupita m’miseu ya Aroma, ndipo anadutsam’malo okwela mumzinda wa Fulugiya, ndi kulo-wela cakumpoto kenako kumadzulo. Motsogolele-dwa ndi mzimu woyela wa Mulungu, io anafikaku Torowa. Kumeneko anakwela bwato ndi ku-pita ku Makedoniya. (Machitidwe 16:6-12) Ntha-wi yonseyo, Paulo anaona kuti Timoteyo analikuwathandiza kwambili, cakuti anam’siya ku Be-reya pamodzi ndi Sila. (Machitidwe 17:14) Pantha-wi ina, Paulo anatuma mnyamatayo ku Tesalonika.Kumeneko, Timoteyo analimbikitsa Akristu okhulu-pilika potsatila zimene anaphunzila kucokela kwaamishonale anzake.—1 Atesalonika 3:1-3.

� Paulo anapempha Timoteyo kuti adulidwe, ndipo iye anavomeleza,osati cifukwa cakuti cinali ciyeneletso kwa Akristu, koma cifukwa ca-kuti Paulo sanafune kuti Ayuda amene anali kuwalalikila azimutsutsacifukwa coyenda ndi mnyamata amene atate ake anali munthu waku-nja.—Machitidwe 16:3.

14 NSANJA YA MLONDA

Patapita nthawi, Paulo analemba za Timoteyokuti: “Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene anga-samaledi za inu moona mtima.” (Afilipi 2:20) Mbiliyabwino imeneyo sinangobwela mwangozi. Timoteyoanakhala ndi mbili yabwino cifukwa cogwila nchitomwakhama, kudzicepetsa, ndi kupilila mokhulupili-ka panthawi zovuta. Cimeneci ndi citsanzo cabwinokwambili kwa acinyamata masiku ano. Dziwani kutipalibemunthuwina amene angakupangileni mbili ya-bwino. Ngati ndinu wacinyamata, muli ndi mwai wa-mtengo wapatali wopanga mbili yabwino mwa kuikaYehova Mulungu pamalo oyamba, ndiponso mwa ku-citila ena zabwino ndi kuwalemekeza.

“UCITE CILICONSE COTHEKAKUTI UBWELE KWA INE”Timoteyo anagwila nchito ndi mtumwi Paulo, bwe-

nzi lake, kwa zaka zoposa 14. Iye pamodzi ndi Pau-lo anakumana ndi zoopsa zambili pa utumiki wao,komanso madalitso ambili. (2 Akorinto 11:24-27)Panthawi ina, Timoteyo anaikidwa m’ndende cifu-kwa ca cikhulupililo cake. (Aheberi 13:23) Ndiponsoiye ndi Paulo anali kukonda ndi kudela nkhawa aba-le ndi alongo ao Acikristu. N’cifukwa cake Pauloanalembela Timoteyo kuti: ‘Ndimakumbukila misoziyako.’ (2 Timoteyo 1:4) Mofanana ndi Paulo, zione-ka kuti Timoteyo anaphunzila ‘kulila ndi anthu ame-ne akulila,’ n’colinga cakuti awatonthoze ndi kuwa-limbikitsa. (Aroma 12:15) Nafenso tiyenela kucitacimodzimodzi.N’zosadabwitsa kuti m’kupita kwa nthawi,

Timoteyo anakhala woyang’anila wabwino wacikri-stu. Paulo anam’patsa udindo wocezela mipingo kutiaithandize ndi kuilimbikitsa, ndiponso kuika aba-le oyenelela kukhala akulu ndi atumiki othandizamumpingo.—1 Timoteyo 5:22.Paulo anali kum’konda kwambili Timoteyo. Iye

anali kum’patsa malangizo othandiza kwambili. Ana-m’limbikitsa kuti aziyamikila maudindo amene ana-patsidwa, ndi kuti ayenela kupita patsogolo mwakuuzimu. (1 Timoteyo 4:15, 16) AnalimbikitsansoTimoteyo kuti sayenela kulola unyamata wake, mwi-nanso manyazi kumulepheletsa kukhala wolimbamtima pocita zinthu zoyenela. (1 Timoteyo 1:3; 4:6,7, 11, 12) Paulo anam’patsanso malangizo othandi-za okhudza matenda ake a m’mimba amene analikumuvutitsa.—1 Timoteyo 5:23.

Paulo anadziwa kuti anali pafupi kuphedwa.Conco, mouzilidwa iye analembela Timoteyo kalatayomaliza. M’kalatayo, munali mau akuti: “Ucite ci-liconse cotheka kuti ubwele kwa ine posacedwa.”(2 Timoteyo 4:9) Paulo anali kum’konda kwambi-li Timoteyo cakuti anali kumuchula kuti “mwanawanga wokondedwa ndi wokhulupilika mwa Ambu-ye.” (1 Akorinto 4:17) N’cifukwa cake, Paulo anafu-na kuti mnzake akhale pafupi naye pamene anatsalapang’ono kufa. Aliyense wa ife ayenela kudzifu-nsa kuti, ‘Kodi anthu amamasuka kundipempha kutindiwathandize akakumana ndi mavuto?’Kodi Timoteyo anapita kwa Paulo panthawi yake?

Sitikudziwa. Koma cimene tidziwa n’cakuti Timoteyonthawi zonse anali kucita zimene angathe kuti ato-nthoze ndi kulimbikitsa Paulo ndi anthu ena. Timo-teyo anali kucita zinthu mogwilizana ndi tanthau-zo la dzina lake limene limatanthauza kuti, “MunthuAmene Amalemekeza Mulungu.” Ndipo iye anapele-ka citsanzo cabwino kwambili ca cikhulupililo cime-ne ife tonse tifunika kutsanzila, kaya ndife acinyama-ta kapena acikulile. ˇ

Ali wacinyamata, Timoteyo anadzipelekakuyamba utumiki wacikristu

Na. 1 2016 15

ZIMENE BAIBO

IMAPHUNZITSA

M’ceni-ceni

wp

16

.1-C

IN1

51

12

0

Kodi akufa adzakhalansondi moyo?Yehova Mulungu ndiye Kasupe wa moyo. (Salimo36:9) Ndiye cifukwa cake m’pomveka kuti iye adzauki-tsa akufa. Baibulo limatitsimikizila kuti Mulungu adza-citadi zimenezi mtsogolo. (

ˆWelengani Machitidwe

24:15) Nanga n’cifukwa ciani adzaukitsa akufa?Colinga ca Mlengi wathu poyamba cinali caku-

ti anthu akhale ndi moyo wosatha padziko lapa-nsi. (Genesis 1:31; 2:15-17) Colinga cake cimene-ci sicinasinthe. Iye zimam’pweteka kwambili akaonakuti anthufe tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana,komanso kuti tili ndi moyo waufupi.—

ˆWelengani Yobu

14:1, 14, 15.

Kodi amene adzaukitsidwaadzakhala kuti?Kodi Mulungu analenga anthu kuti azikhalakumwamba? Iyai. Mulungu analenga angelo kutiazikhala kumwamba. Koma anthu anawalengakuti azikhala padziko lapansi. (Genesis 1:28;Yobu 38:4, 7) Mwacitsanzo, ganizilani anthu ame-ne Yesu anaukitsa. Iwo ataukitsidwa, anakhalansondi moyo padziko lapansi. Conco, anthu ambili ame-ne adzaukitsidwa adzakhalanso ndi moyo padzikolapansi.— ˆ

Welengani Yohane 5:28, 29; 11:44.Komabe, Mulungu anasankha anthu ocepa kuti

adzakhale kumwamba ndipo adzapatsidwa matupiauzimu. (Luka 12:32; 1 Akorinto 15:49, 50) Anthuamene adzaukitsidwila kumwamba adzalamulila dzikolapansi limodzi ndi Yesu.—

ˆWelengani Chivumbulutso

5:9, 10.

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

WELENGANI MAYANKHO A MAFUNSOENA A M’BAIBULO PA INTANETI

KUKAMBA ZOONA, MLENGI WA MOYOADZAUKITSADI AKUFA

Kuti mudziwezambili, onaninkhani 7 m’buku ili,lofalitsidwa ndiMboni za Yehova

Mungatengebuku limeneli pawww.jw.org

Nditumizileni buku laZimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceniCINENELO ������������������������������������������������������������������������

DZINA �������������������������������������������������������������������������������

ADILESI ����������������������������������������������������������������������������

�����������������������������������������������������������������������������������������

�����������������������������������������������������������������������������������������

�����������������������������������������������������������������������������������������

Onani tsamba 2 kuti mudziwe adilesi ya kumenemungalembele kalata

sMungatenge magaziniino ndi enanso akalekwaulele pa intaneti

Baibulo limapezekapa intanetim’zinenelopafupifupi 100

Pitani pa webusaiti ya jw.orgkapena citani sikani cidindoici ngati muli ndi foni kapenacipangizo cina cimenecingacite sikani

no

p