Khanda ndi Mphatso. Lipatseni Mwayi. - Healthy Newborn ...

40
1 COVER Muuni wa Alangizi a khanda ndi Mphatso (Facilitator Guide) Khanda ndi Mphatso. Lipatseni Mwayi.

Transcript of Khanda ndi Mphatso. Lipatseni Mwayi. - Healthy Newborn ...

1

COVER

Muuni wa Alangizi a khanda ndi Mphatso

(Facilitator Guide)

Khanda ndi Mphatso. Lipatseni Mwayi.

Phukusi la alangizi a Khanda ndi Mphatso linapangidwa ndi Unduna wa zaumoyo mogwirizana ndi bungwe Save the Children , pamodzi ndi anthu ndi mabungwe ena monga Mercantile International, ADECOTS, ndi Center for Development Communication. Cholinga cha phukusili ndi kuthandizira kupititsa patsogolo uchembere wabwino komanso umoyo wa makandaku Malawi.

3

Kalata yowalandira alangizi a Khanda ndi Mphatso

Okondedwa Alangizi,

Ngati mukuwerenga kalatayi, ndiye kuti mwasankhidwa kukhala mlangizi wa khanda ndi Mphatso, kampeni imene cholinga chake ndi kupulumutsa miyoyo ya makanda ku Malawi. Munasankhidwa kukhala mlangizi wa khanda ndi mphatso chifukwa muli ndi kuthekera koti mutha kusintha maganizo, chikhalidwe, zikhulupiliro ndi mchitidwe wa anthu mdera lanu. Pokhudzana ndi kampeniyi, tikuyembekezera kuti mutengapo mbali kusintha maganizo, chikhalidwe, zikhulupiliro ndi mnchitidwe wa amayi oyembekezera,amayi omwe abadwitsa anakumene, amuna komanso abale awo pa nkhani ya makanda.

Malawi ndi dziko limodzi mwa mayiko omwe chiwerengero cha ana omwe amafa chifukwa chobadwa osakwana masiku ndi chachikulu kwambiri, angakhale Malawi linali dziko limodzi mwa mayiko omwe anali oyamba kupereka chisamaliro cha Kangaro kwa anawa. Zina mwazifukwa zomwe zimapangitsa chiwerengerochi kuti chichuluke ndi zinthu mchitidwe onyozetsa ana osakwanamasiku, kusadziwa zambiri za ana amenewa ndi chisamaliro choyenelera kuwapatsa, komanso kusowekera chithandizo kuchokera kwa okondedwa, achibale ngakhale anthu ena a mmudzi posamalira khanda losakwana masiku. Ndi cholinga cha alangizi a Khanda ndi Mphatsa kutengapo mbali potsogolera kuthana ndi zipsinjo zimenezi.

Zipangizo zimene ziri mu phukusili zinapangidwa ndicholinga chokuti zikakuthandizireni kugwira ntchito yopititsa patsogolo moyo wamakanda mu dera lanu. Zipangizo zimenezi zikuthandizani inu kuti mudziwe zambiri, komanso zikuthangatani kutsogolera zokambirana zokhudza kasamalidwe kabwino ka mimba, kukonzekera kubereka komanso kusamalira ana obadwa masiku osakwana mu njira ya kangaroo,zomwe muzichita ndi anthu omwe mukuwathandiza mu chipatala,makamaka amayi omwe ndioyembekezera,amayi omwe abadwitsa makanda osakwana masiku, okondedwa ndi achibale awo ena, komanso amayi, abambo,mabanja ndi anthu ena onse amudera lanu.

Tikukuthokozani kwambiri povomereza kutenga nawo mbali mu kampeni imeneyi yosamalira komanso kupititsa patsogolo miyoyo yamakanda ang’ono kuti athandizike kukula mwa thanzi ndi kukhala nzika zodalirika m’malawi.

KHANDA NDI MPHATSO,

LIPATSENI MWAYI

4

Zambiri zokhudza Phukusi la Alangizi a Khanda ndi Mphatso

Phukusili lapangidwa kuti lithandzire alangizi a khanda ndi Mphatso kugwira ntchito yopititsa patsogolo moyo wamakanda mu dera lawo, kudzera mu zokambirana ndi anthu. Zokambiranazi cholinga chake ndi kupititsa patsogolo moyo wathanzi wa amayi ammimba ndi makanda, komanso kudziwitsa anthu zambiri za ubwino wosamalira ana osakwana masiku mu njira ya Kangaroo. Cholinga cha phukusili maka maka ndikuthandzira kuti anthu atengepo mbali polimbana ndi ziphinjo zosiyana siyana zomwe zimapititsa pansi miyoyo ya makanda, maka maka osakwana masiku. Ndi cholinga cha phukusili kusintha zikhalidwe ndi zikhulupiro, komanso kulimbikitsa abambo kuti atenge nawo mbali posamalira moyo wa amayi a mimba ndi makanda.

Zipangizo zimene ziri muphukusili zikathangata alangizi kutsogolera zokambirana zokhudza kasamalidwe kabwino ka mimba, kukonzekera kubereka komanso kusamalira ana obadwa masiku osakwana mu njira ya kangaroo, zomwe alangizi akachite ndi anthu omwe akuwathandiza mu chipatala,makamaka amayi omwe ndioyembekezera,amayi omwe abadwitsa makanda osakwana masiku, okondedwa ndi achibale awoena, komanso amayi, abambo,mabanja ndi anthu ena onse amudera lanu. Zipangizozi zapangidwa moti alangizi atha kukagwiritsa ntchito muzokambirana ndi anthu a mitundu yonse, ngakhale amene sangathe kuwerenga.

Zolinga za Phukusi la Alangizi a Khanda ndi Mphatso

Phukusili linapangidwa ndi cholinga choti ogwiritsa ntchito akachite izi:

JJ Adziwe udindo wao popititsa tsogolo moyo wa thanzi wa amayi oyembekezera ndi makanda kudzera mu kampeni ya khanda ndi mphatso

JJ Adziwe udindo wao pothandizira kuthetsa zikhulupiliro, zikhalidwe ndi mchitidwe omwe umapititsa pansi umoyo wa thanzi wamakanda

JJ Adziwe kagwiritsidwe ntchito ka zipangizo za mu phukusili zomwe zapangidwa kuti ziwathangatire kutsogolera zokambirana ndi anthu mu dera lawo

JJ Athe kupereka ma uthenga ukwanira 4 kapena 6 okhudzana ndi kampeni ya Khanda ndi Mphatso

JJ Akhale okonzeka ndi kuthekera kutenga mbali ngati mlangizi wa Khanda ndi mphatso mudera lawo

JJ Aphunzire ndi kumvetsetsa zoyenera kuchita pamene akukambirana ndi anthu

5

Zipangizo za mu phukusi la alangizi a Khanda ndi Mphatso

Phukusili liri ndi zipangizo zisanu ndi ziwiri (7) zomwe ziri ndi nkhani ndi uthenga okhudzana ndi uchembere wabwino, moyo wa thanzi wa makanda komanso chisamaliro cha Kangaroo kwa ana osakwanamasiku:

JJ Flipchart yophunzitsira za Kangaroo

JJ Khani za Chiyembekezo zolimbikitsa Kangaroo

JJ Masewero a Khanda ndi Mphatso

JJ Nyimbo ya Khanda ndi Mphatso (ya pa wayilesi ndi kanema)

JJ Uthenga wa Khanda ndi Mphatso (radio spots)

JJ Kalendala ya Khanda ndi Mphatso

JJ Muuni wa kagwiritsidwe ntchito kaphukusi la alangizi aKhanda ndi Mphatso

Mu phukusiri muli chowunikira/muuni wolozera m’mene chipangizo chiri chonse chingagwiritsidwire ntchito pokambirana ndi anthu osiyana siyana. Tayikamonso Badge yomwe tiri ndi chikhulupiliro kuti muziyivala nthawi zonse zomwe mukutsogolera zokambirana ndi anthu, kapena mukugwira ntchito zokhudzana ndi Khanda ndi Mphatso. Badge yi ithandizira kuti anthu akuzindikireni inu ngati mlangizi wa Khanda ndi Mphatso.

6

Zamkatimu

Kalata yowalandira alangizi a Khanda ndi Mphatso _______________ 3

Zambiri zokhudza Phukusi la Alangizi a Khanda ndi Mphatso ______ 4

Zolinga za Phukusi la Alangizi a Khanda ndi Mphatso ____________ 4

Zipangizo za mu phukusi la alangizi a Khanda ndi Mphatso _______ 5

Zamkatimu ________________________________________________ 6

Kodi Kangaroo ndi chiyani? _________________________________ 9

Muuni wa Kagwiritsidwe ntchito ka Flip Chart __________________ 10

Muuni wa Kagwiritsidwe ntchito ka Nkhani za Chiyembekezo _____ 15

Muuni wa Kagwiritsidwe ntchito ka Masewero a Khanda ndi Mphatso ______________________________________________ 19

Muuni wa Kagwiritsidwe ntchito ka Nyimbo ya Khanda ndi Mphatso _____________________________________________ 26

Kagwiritsidwe ntchito ka Kalendala ya uthenga wa chisamaliro cha ana osakwana masiku __________________________________ 29

Malangizo Othandizira Kulankhula Ndi Anthu __________________ 30

Zipangizo zina ____________________________________________ 32

Zambiri Zokhudzana ndi Uchembere wabwino, Umoyo wa Makanda ndi Chisamaliro cha ana osakwana masiku ___________ 33

7

Cholinga cha bukhuli ndi kuwunikira alangizi a Khanda ndi Mphatso kagwiritsidwe ntchito ka Phukusipa la zipangizo.

Pa chipangizo chiri chonse chomwe chayikidwa mu phukusili, mupeza muuni omwe ali mafunso komanso malangizo okuthandizirani pa zokambirana zanu. Khalani omasuka kugwiritsira ntchito mafunso onse kapena ena mwamafunsuwa pokuthandizirani kuyambitsa zokambirana ndi anthu. Muthanso kupanga mafunso anu mokhudzana ndi nkhani kapena uthenga omwe mukupereka tsiku limenelo, omwe angathe kukuthandzirani kuti anthu omwe mukukambirana nawo athe kukamba nkhani zawo zokhudzana ndi chisamaliro chamwana.

Tsatirani ndondomeko iri m’musiyi pamene mwakumana ndi anthu oti mukambirane nawo:

Kagwiritsidwe Ntchito Ka Bukhuli

1. Alonjereni anthu omwe mukufuna kukambirana nawo

2. Awuzeni zolinga za zokambirana za tsiku limenelo

3. Afunseni anthu omwe mutakambirane nawo za mbiri ya moyo wawo (mwachitsanzo: ali ndi zaka zingati? Ali pa banja? Ali ndi ana angati?)

4. Mukamaliza zokambirana, athokozeni anthu ndipo alimbikitsenikuti azakhalepo pa zokambirana zotsatira

Kugwiritsa ntchito Zipangizo

Onetsetsani kuti mukudziwa bwino kagwiritsidwe ntchito ka zida zimene ziri mu phukusili moyenerela.

Gwiritsani ntchito zipangizo zoyenelera zokuti zikuthandizireni kutsogolera zokambirana ndi anthu. Mutha kugwiritsa ntchito fl ip chart, masewero a pa wailesi, nkhani za anthu zomwe ziri pa CD, kapena Nyimbo ya khanda ndi Mphatso.

Kugawa Nthawi Moyenerela

1. Ganizirani kuti zokambiranazi zingatenge nthawi yayitali bwanji

2. Siyani nthawi ina yoti muunikire mwachidule ndi kutsindikiza mfundo zomwe mwakambirana ndi kugwirizana.

8

Zochitika Pagulu

Pagulu lirilonse, onetsetsani kuti aliyense:

Mafunso Otsogolera zokambirana

Musanayambe kupereka uthenga, mukuyenera kumva zomwe anthu akuganiza pankhani kapena uthenga omwe uli mu zipangizo zomwe mukugwiritsa ntchito, komanso zomwe anthu akudziwa kapena amachita m’dera lawo. Izi zikuthandizani kuti mudziwe zoyenera kutsindika. Funsani izi:

1. Wamvetsetsa zochitika zonse

2. Ali omasuka kunena maganizo awo

3. Ali olimbikitsidwa kupereka nawo maganizo awo

4. Ali ndi mwayi otenga nawo mbali

5. Akumvera ndi kulemekeza maganizo a anzawo otenga nawo mbali

1. Mukuganiza zotani pa nkhaniyi kapena uthengawu?

2. Mwakondamo chani mu nkhaniyi kapena uthengawu?

3. Mwaphunziramo chani?

4. Chiripo chomwe mwamva kapena kuona mu nkhaniyi kapena uthengawu chomwe mungafune mutadziwa zambiri?

Mauthenga

Mukamva/mukazindikira zomwe anthu akudziwa kapena amachita, perekani ma uthenga oyenelera pa peji lomwe mukugwiritsa ntchito tsiku limenelo

Kuchitapo Kanthu

Pomalizira pa zokambirana, fotokozani mwachidule mfundo zofunikira, ndipo alimbikitseni anthu kuchitapo kanthu pa uthenga omwe mwakambirana. Ngati pali yoti ikonzedwe, lembani amene asankhidwa kuti agwire ntchito imeneyi, nthawi yomwe ntchito itagwiridwe, mmene itagwiridwire, komanso nthawi imene adzapereke zotsatira za gulu.

9

JJ Kangaroo ndi chisamaliro chopatsidwa kwa mwana obadwa masiku osakwana chimene mwana amayikidwa pa chifuwa pakholo lake kuti alandire kutentha, chakudya, chitetezo kuti ziwalo zake zikhwime.

JJ Mwanayu amabadwa ziwalo zonse zosakhwima ndipo afunika kupatsidwa kutentha, chakudya, chitetezo potsatira njira ya kangaroo.

JJ Mwana akangobadwa amayikidwa amayikidwa pachifuwa cha kholo lake kuti thupi lawo ligundane ndikugawana kutentha.

JJ Mwana osakwana masiku amafunika:

1. Kumuthandizira kumumwetsa mkaka wa mmawere.

2. Kumuyang’anira ndi kumuyeza pafupipafupi.

Ubwino wogwiritsa njira ya kangaroo kwa mwana obadwa masiku osakwana

1. Mwana amalandira chifundizi chokwanira nthawi zonse.

2. Mwana amadyetsedwa mokwanira

3. Imalimbikitsa Chikondi cha kholo pa mwana.

4. Mwana amatetezedwa kumatenda ndi mavuto osiyanasiyana.

5. Amatulutsidwa msanga kuchipatala chifukwa mwana amakwaniritsa msanga zifukwa zotulutsidwira mwachangu choncho amatha kusamalira zina zapakhomo.

KODI KANGAROO NDI CHIYANI? 1

10

MUUNI WA KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA FLIP CHART2

Nkhani Ya Maliyatu Ndi Patuma

Maliyatu ndi kachiphadzuwa m’mudzi wa Kankhomba ku Machinga. Sanangokhala chiphadzuwa, kusukulunso ndiwanzeru moti tikunena pano akuchita ma phunziro a ukachenjede ku sukulu yaku Zomba. Maliyatu ali ndi nzake wa pa mtima, Patuma, yemwe anabereka mwana osakwana masiku. Maliyatu akumunyogodola mwana wa Patuma chifukwa chokuti ndi wamng’ono kwambiri, iye akuona ngati kuberekamwana osakwana masiku ndi chilango kwa Patuma, komanso akuganiza kuti mwanayu sakhala moyo chifukwa wabadwa masiku osakwana. Koma amayi ake a Maliyatu amudzudzula ndikummuza kuti kubereka mwana osakwana masiku sichilango, komanso khanda lingachepe bwanji, ndi mphatso; lofunika kulipatsa mwayi okhala ndi moyo wathanzi komanso tsogolo lowala polisamalira. Iwo apitililza kumufotokozera kuti mwa ana 4 amene anabereka, m’modzi anabadwa osakwana masiku koma onse ali moyo ndipo onse anakula mosilirika chimodzi modzi”.

Flip chart ili ndi makhadi asanu omwe akufutokoza nkhani ya Maliyatu, yokhudzana ndi chisamaliro cha ana osakwana masiku cha Kangaroo.

M’musimu muli nkhani yomwe ili mu fl ip chart mu mwachidule. Pa fl ip chart po, muona kuti kuseli kwa khadi iri yonse yomwe iri ndi chithunzi, pali mafunso angapo otsogolera zokambirana, komanso uthenga okuthandizirani kutsindikiza mfundo zokambirana pa khadi ili yonse. Khalani omasuka kugwiritsa ntchito onse kapena ena mwa mafunsowa poyambitsa zokambirana ndi anthu. Khalani omasuka kugwiritsira ntchito mafunso onse kapena ena mwamafunsuwa pokuthandizirani kuyambitsa zokambirana ndi anthu. Muthanso kupanga mafunso anu mokhudzana ndi nkhani kapena uthenga omwe mukupereka tsiku limenelo

11

Maliyatu anachita chidwi ndipo anafunitsitsa kuti amve zinakhala bwanji kuti mai ake abereke mwana osakwana masiku ndipo ndi ndani mwa abale ake atatuwo poti onse amaoneka alunga lunga ndipo ndi a nzeru

Mai a Maliyatu anafotokozera mmene matenda anawayambira atangoyamba mwezi wa chisanu ndi chiwiri (7) wa pathupi pa mwana ameneyu, komanso mmene bamboo ake anathandizira kusamala mwana ameneyu kuti akule mwa thanzi. Anafotokoza kuti ngakhale anali okhumudwa atabereka kamwana kolemera ngati paketi imodzi ya sugar (1kg), iwo pamodzi ndi bambo ake anachilimika usiku ndi usana kulandizana kufungatira mwana pa Kangaroo angakhale zinali zovuta chifukwa anthu ambiri amawanyogodola,

Atamva izi Maliyatu anawathokoza amayi ake chifukwa cha ntchito yomwe anagwira kusamalira m’modzi mwa abale ake mpaka kukula, ndipo anafunsitsakuti adziwe kuti ndi ndani chifukwa palibe mwa azibale ake amene amauonekera motero. Mayi a Maliyatu anamukumbatira mwana wawo ngati mwa Kangaroo kumene, ndikumuyankha funso lake, “Maliyatu mwana wanga wa pamtima, ndiwe amene unabadwa masiku osakwana. Chikondi cha atate ako ndi ine chinaonekera pa iwe. Patuma tikuyenera kumuthandiza kulera mwana amene uja kuti akule wathanzi ndinso wanzeru”

Maliyatu anali odzidzimuka ndi nkhani imeneyi, ndipo anawakumbatira amayi ake ndi chimwemwe pozindikira Chikondi chomwe anamupatsa. Maliyatu analonjeza kukamuthandiza Patuma ndi kumulimbikitsa kusamalira mwana wake mu njira ya Kangaroo.

Kagwiritsidwe Ntchito Ka Flip Chart

Pa peji ili yonse mupeza mafunso ndi malangizo okuthandizirani mu zokambirana zanu. Khalani omasuka kugwiritsira ntchito mafunso onse kapena ena mwamafunsuwo pokuthandizirani kuyambitsa zokambirana ndi anthu. Muthanso kupanga mafunso anu mokhudzana ndi nkhaniyi, omwe angathe kukuthandizirani kuti anthu omwe mukukambirana nawo athe kukamba nkhani zawo zokhudzana ndi chisamaliro chamwana.

Pa peji iliyonse kapena Zokambirana zonse, chitani izi:

1. Onetsetsani kuti anthu akona zithunzi ndipo inu muli mbali ya malemba

2. Funsani okambirana nawo kuti akuuzezi zimene akuona pachithunzipo

3. Afotokezereni nkhani ya Maliyatu yomwe iri pa peji imeneyo

4. Kambiranani ndi anthu pa zomwe zimachitika m’dera lawo zokhudza nkhaniyo

12

Za Mkati Mwa Flip Chart

Ndondomeko ya Zokambirana

Nkhani ya Maliyatu

JJ Afotokozereni anthu nkhani yamaliyatu mokhudzana ndi chithunzi chomwe akuona tsiku limenelo

Mafunso Otsogolera

JJ Musanayambe kupereka uthenga, mukuyenera kumva zomwe anthu akuganiza pankhani ya Maliyatu, komanso zomwe anthu akudziwa kapena amachita m’dera lawo. Izi zikuthandizani kuti mudziwe zoyenera kutsindika. Funsani izi:

1. Mukuganiza zotani pa nkhaniyi?

2. Mwakondamo chani mu nkhaniyi?

3. Mwaphunziramo chani?

4. Chiripo chomwe mwamva munkhaniyi chomwe mungafune mutadziwa zambiri?

Mauthenga

JJ Mukamva/mukazindikira zomwe anthu akudziwa kapena amachita, perekani ma uthenga oyenelera pa peji lomwe mukugwiritsa ntchito tsiku limenelo

Kuchitapo Kanthu

JJ Alimbikitseni anthu kuchitapo kanthu pa uthenga omwe mwakambirana.

Khadi Loyamba

JJ Patuma, mzake wa maliyatu ndi oyembekezera.

Mfundo Zokambirana: Zoyenera kuchita pamene amayi akuyembekezera

Khadi lachiwiri

JJ Patuma apita limodzi ndi mamumana wake mavhiho ku sikelo ya amayi oyembekezera.

Mfundo Zokambirana: Abambo atenge mbali, ubwino wasikelo ya amai oyembekezera, zinthu zofunikira kwambiri kuzidziwa banja likakhala loyembekezera

13

Khadi lachitatu

JJ Mfundo zokambirana: Zizindikiro zoopsya za mimba, Zizindikiro za nthawi yochira, Kupita ku sikelo ya amayi oyembekezera

Khadi Lachisanu

JJ Maliyatu atamva kuti nzake Patuma wabereka mwana osakwana masiku, anapita pamodzi ndi mayi ake kukamuona ndipo anali odabwa kuona Patuma akusamalira mwana wake mu njira ya Kangaroo

Mfundo Zokambirana: Ubwino wa Kangaroo

Khadi lachinayi

JJ Patuma ndi Mavhiho alandira uphungu kuchokera kwa a namwino pa mmene angasamalire mwana wao osakwana masiku mu njira ya kangaroo.

Mfundo Zokambirana: Kangaroo ndi chiyani, ndondomeko ya Kangaroo

Khadi lachisamu ndi chimodzi

JJ Mai a Maliyatu ndi mamuna wa Patuma, Mavhiho, akumuthandiza Patuma kusamalira mwana mu njira ya Kangaroo

Mfundo Zokambirana: Udindo wa mwamuna ndi anthu ena posamalira mwana osakwana masiku

Khadi la chisanu ndi chiwiri

JJ Atachoka kokamuona mwana wa Patuma, maliyatu ayamba kunyogodola mwana wa patuma chifukwa ndi wamng’ono kwambiri, ndipo Mai ake amuuza kuti mmodzi mwa ana awo 4 anabadwa osakwana masiku koma anakula ndi thanzi komanso mosilirika ngati ena onse. Izi zimudabwitsa Maliyatu kwambiri.

Mfundo Zokambirana: Kulimbitsa kutsatira njira ya Kangaroo, Kuthana ndi nkhambakamwa

Khadi lachisanu ndi chitatu

JJ Mai a Maliyatu afotokoza zomwe iwo ndi bambo a Maliyatu anadutsamo atabereka mwana osakwana masiku

Mfundo Zokambirana: Ndi udindo wa aliyense kuthandizira kulera mwana mu njira ya Kangaroo, Zimene anthu angachite pothandizira kulera mwana mu njira ya Kangaroo

14

Khadi la chisanu ndi chinayi

JJ Mai a Maliyatu amufotokozera Maliyatu za mbali yayikulu yomwe bamboo ake anatenga posamalira mwana wao osakwana masiku

Mfundo Zokambirana: Kulimbikitsa kumasukirana mbanja pa maleredwe a mwana, Kukhala okonzeka, kulimbitsa abambo kutenga mbali.

Khadi la chikhumi

JJ Mayi a Maliyatu amuuza mwana wao kuti iyeyo ndi amene anabadwa masiku osakwana, zimene zamudzidzimutsa Malaiyatu chifukwa sanayembekezere konse. Maliyatu alonjeza kukamuthandiza Patuma ndi kumulimbikitsa kusamalira mwana wake mu njira ya Kangaroo.

Mfundo zokambirana: Kubereka khanda losakwana masiku si chilango, Khanda losakwana masiku ndi munthu ngati wina aliyense, Ana osakwana masiku amakula mwanthanzi ndi nzeru ngati asamaliridwa mu njira ya kangaroo

14

15

MUUNI WA KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA NKHANI ZA CHIYEMBEKEZO 3

Nkhani za chiyembekezo zomwe zayikidwa mu phukusili ndi nkhani zochokera kwa anthu omwe anavomereza kugawirana nafe nkhani za moyo wawo zokhudzana ndi ana osakwana masiku, komanso zolimbikitsa njira ya kangaroo kwa ana osakwana masiku. Chonde dziwani kuti mayina awo asinthidwa poteteza chinsinsi chawo. Anthu onsewa anadutsako muziphinjo zobereka ndi kusamalira mwana osakwana masiku, onsewa anagwiritsa ntchito njira ya kangaroo kusamalira ana awo ndipo zinawapindulira poti ana awo anakula athanzi ndi anzeru. Khalani tcheru ndi kumvera nkhani zawo pamene akufotokoza ziphinjo zomwe anadutsamo posamalira ana awo mu njira ya Kangaroo, komanso kugawana nafe zomwe anachita pothana ndi ziphinjo zimenezo ndi kupulumutsa miyoyo ya ana awo

Mmusimu muli nkhani za anthuwa mwachidule, komanso mafunso omwe apangidwa othandizira kutsogolera zokambirana ndi anthu akamaliza kumvera nkhani iri yonse.

Nkhanizi mutha kusewera kwa amayi kapena mabanja omwe abereka mwana osakwana masiku pamodzi ndi achibale awo kuti akalimbikitsidwe. Muthanso kusewera nkhanizi kwa anthu, ma gulu kapena mu zochitika zina za m’mudzi kuti zikathandizire kuthetsa nchitidwe onyogodola ana osakwana masiku.

16

Chimwemwe anabeleka mwana osakwana masiku ali ndi zaka 14. Iye anavutika muntima kuti avomereze zoti wabereka mwana osakwana masiku komanso wamng’ono kwambiri, makamaka chifukwa cha nkhamba kamwa zomwe anamva zokhudzana ndi ana osakwana masiku. Zimenezi zinamupangitsa Chimwemwe kuti ataye chikhulupiliro chokuti mwana wake apulumuka. Mverani kuti mumve zomwe zinachitika atachilimika kusamalira mwana wake kudzera mu njira ya kangaroo monga mwa malangizo a ku chipatala. Mu nkhaniyi mumvanso zimene iye anachita pothana ndi kunyogodola komanso nkhamba kamwa zomwe anakumana nazo m’mudzi mwao zokhudza mwana wake osakwana masiku. Kodi Chimwemwe anachita chiyani kusamalira mwana wake kuti mpaka akule nkukhala mwana wa thanzi komanso osilirika?

Nkhani ya chimwemwe

Nkhani ya Juliet

Nkhani ya Matilida

Nkhani ya abusa a Makawa

Juliet anabereka ana amapasa omwe anabadwa masiku osakwana. Motsatira malangizo a ku chipatala, iye anawasamalira ana ake mwachikondi kudzera mu njira ya kangaroo, mpaka onse anakula mosilirika. Juliet anachita izi ndi chithandizo chochokera kwa abale ake komanso kwa a namwino kuchipatala.

Aka kanali ka chitatu kuti Matilida abereke mwana osakwana masiku. Ana oyamba omwe Matilida anabereka kawiri konse asanakwane masiku anamwalira. Atabereka mwana wina osakwana masiku kachitatu, Matilida anali ndi mantha komanso nkhawa ngati mwana wake atakhale ndi moyo, koma iye pamodzi ndi mamuna wake analimbikira kusamalira mwana wao mu njira ya Kangaroo mpaka anakula ndithu. Khalani tcheru kuti mumvere mmene Matilida ndi mamuna wake anathanirana ndi zonyoza komanso zonyogodola mwana wao.

Mwana wa chisanu ndi chitatu wa a busa a Makawa anabadwa osakwana masiku. Ngakhale abusa a Makawa anali mtsogoleri wa mpingo waulemu wawo, anthu a m’mudzi mwao anawanyogodola iwo ndi banja lawo chifukwa chokuti anabereka mwana osakwana masiku ndipo amachita Kangaroo. Khalani tcheru kuti mumve kuti Chisamaliro cha Kangaroo zinathandiza bwanji banja la abusa a Makawa kuti mwana wao osakwana masiku apulumuke.

17

A phiri ndi bambo wabwino wa ana awiri, komanso mamuna wa Chikondi ndi akazi awo. Iwo akufotokoza nkhani ya m’mene akazi awo anaberekera ano awo amapasa masiku asakwane. Khalani tcheru kuti mumvere m’mene abanja la aPhiri linathanirana ndi nkhamba kamwa za m’mudzi komanso malangizo omwe a Phiri akupereka kwa abambo anzawo mokhudzana ndi ana osakwana masiku komanso chisamaliro choyenera cha Kangaroo.

Nkhani ya aPhiri

Nkhani ya a nesi (a namwino) a Jana

Mafunso Otsogolore zokambirana za Nkhani za chiyembekezo

A namwino a Jana, anabadwa osakwana masiku, komanso nawo anabereka mwana osakwana masiku yemwe anakulapano ndi kamyamata ndithu, ndipo akhala akugwira ntchito yothandiza ndi kulimbikitsa mabanja kusamalira ana osakwana masiku mu njira ya kangaroo. A Jana akufotokoza momwe akhala akuthandizira ana osiyana siyana osakwana masiku omwe awona akupulumuka, ndikukula kukhala ana a thanzi komanso osilirika. Tiyeni timvere nkhani yi kuti tilimbikitsike kuti ana, ngakhale atabadwa mosakwana masiku, ndi mphatso ndipo ayenera kupatsidwa mwayi popatsidwa chisamaliro choyenera.

Munsimu muli ena mwa mafunso omwe mutha kufunsa potsogolera zokambirana ndi anthu pamene amaliza kumwera nkhani iri yonse. Chonde gwiritsani ntchito mafunsowa kutsogolera zokambirana zanu ndipo onetsetsani kuti anthu ali omasuka kupereka maganizo awo. Pamene mukukambirana, akumbutseni anthu kuti palibe yankho lolondora kapena lolakwa, aliense akhale omasuka kupereka maganizo kapena nkhani yake. Ndi udindo wa alangizi kukonza zonse zisali zolondola pomaliza pa zokambirana.

1. Maganizo anu ndiotani pa nkhaniyi? Mukumva bwanji?

2. Kodi munthu amene akukamba nkhani yakeyo, akukumbutsani wina wake yemwe mumadziwa? Tiuzeni zambiri.

3. Nkhani yangati yomwe yakambidwayi ikukumbutsani nkhani ina iri yonse? Tiuzeni zambiri?

4. Kodi inu munakakhala eni ake a nkhaniyi, munakatani? Munakathana nazo bwanji zonyogodola kapena kunyoza ana osakwana masiku?

18

5. Maganizo anu ndi otani pa chisamaliro chomwe chimaperekedwa kwa ana osakwana masiku (Kangaroo)? Kodi mukuona ngati mutha kukwanitsa kuchita Kangaroo?

6. Mutakhala kuti mukusamalira mwana osakwana masiku mu njira ya Kangaroo, ndi ndani wapafupi amene mukuona ngati atha kukuthandizani?

7. M’mene mwamvera nkhaniyi, maganizo anu ndi otani pa ana omwe amabadwa osakwana masiku? Nanga maganizo anu ndi otani pa Kangaroo?

8. Pomalizira pa Nkhaniyi tamva kuti Khanda ndi mphatso, liyenera kupatsidwa mwayi. Inu mukagani zokuti zimenezi zikutanthauza chiyani? Mukugwirizana nazo kapena ayi? Chifukwa chiyani?

9. Kodi tingapange chiyani kuti khanda tilipatse mwayi?

19

MUUNI WA KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA MASEWERO A KHANDA NDI MPHATSO4

Takulandirani mu chigawo chimenechi cha sewero la Khanda ndi Mphatso. Amenewa ndi masewero 13 mwamasewero 52 omwe anaseweredwa pa wailesi ku Malawi zaka zapitazo. Masewerowa anakonzedwa ndi a Johns Hopkins University ndi chithandizo chochokera ku USAID udzera mu kampeni ya Moyo ndi Mpamba yomwe anakonza a SSDI-Communication. Masewero 13 omwe akukhudzana ndi nkhani ya uchembere wa bwino ndimoyowa thanzi makanda, asankhidwa ndikukonzedwanso ndichilolezo chochokera ku Johns Hopkins University, ndipo akukupatsirani ndi a unduna wa zaumoyo, mogwirizana ndi bungwe la Save the Children, kudzera mu kampeni ya Khanda ndi Mphatso. Kudzera mu masewero amenewa, omvera aphunzira kuti mwana aliyense, angachepe bwanji, ndi mphatso, ndipo akuyenera kupatsidwa mwayi okula ndi kukhala mzika yodalilirika. Omvera aphunziranso kuti banja lina liri lonse litha kubereka mwana osakwana masiku, sizitengera kuti ena ndiolakwa kapena alandira chilango, zitha kuchitikira wina aliyense. Masewerowa akulimbikitsanso uchembere wabwino, kuti abambo azitengapo mbali pa uchembere wabwino,

20

Anthu omwe ali mu masewero amenewa ndi awa: chonde afotokozereni anthu omwe akumvera masewerowa za anthu amene ali museweroli kuti amvetsetse bwino bwino:

1. Nasilina ndi Richard – ili ndi banja

2. Mai ndi bambo Gama – a neba a Nasilina ndi Richard

3. Esime – anali chibwenzi cha Richard

4. Mai Gwaza – Azakhali a Richard

5. Ndaziona – Mwana wa azakhali a Richard

6. Gibo – Chibwenzi cha Ndaziona

7. Mr. Mauluka – A shuga dadi a Ndaziona komanso abambo a mwana wake

Mukatha kuwafotokozera omvera za anthu omwe ali museweroli, mutha kusewera sewero limodzi limodzi pa wayilesi. Pomaliza pa seweroliri lonse, afunseni omvera mafunso okhudzana ndi zomwe zikuchitika museweromo mokhudzana ndi zolinga za kampeni ya Khanda ndi Mphatso. Mukakhala kuli muli ndi nthawi yambiri kapena yokwanira, mutha kusewera masewero angapo kuti mukambirane ndi anthu zokhudza uchembere wabwino kapena chisamaliromakanda.

M’munsimu muli ena mwa mafunso omwe mungathe kugwiritsa ntchito potsogolera zakambirana ndi anthu. Muthanso kupanga mafunso anu mokhudzana ndi nkhaniyi, omwe angathe kukuthandizirani kuti anthu omwe mukukambirana nawo athe kukamba nkhani zawo za uchembere wabwino kapena chisamaliro cha makanda.

Episode 1:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Kodi mukuganiza kuti Richard amuperekeza Nasilina to the Antenatal clinics?

3. M’mene mwaonera pa zokambirana pakati pa Richard ndi Nasilina, pali ubwino wanji oti abambo ndi amayi azipitira limodzi ku sikelo ya amayi oyembekezera?

4. Kodi amayia atha kuchitapo chiyani kuti abambo azipita nawo ku sikelo ya amayiyoyembekera?

5. Tingachitepo chiyani kuti abambo amvetsetse kufunikira kopita limodzi ku sikelo ya amayi oyembekezera?

21

Episode 2:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Ndi chifukwa chiyani amuna kapena abambo satengapo mbali pa uchembere wabwino, kuphatikizipo kupelekeza akazi awo ku sikelo?

3. Muli ndi zilanginizo zotani m’mudzi wanu zothandizira kuti abambo azitengapo mbali pa uchembere wabwino?

4. Amayi amapeza kuti chithandizo chowathangatira pamene amuna awo sakutengapo mbali pa nkhani ya uchembere wabwino?

Episode 3:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Pali ubwino wanji oti abambo apitire limodzi ku sikelo ndi amayi oyembekezera?

3. Ndi chifukwa chani abambo ndi amayi akuyenera kuyezetsa matenda osiyana siyana limodzi pamene akuyembekezera?

Episode 4:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Pali ubwino otani banja kuyezetsera limodzi ngati ali ndi HIV pamene akuyembekezera?

3. Ndi zifukwa zotani zimene zimapangitsa kuti abambo asapite kukayezetsa matenda ndi amayi pa nthawi yoyembekezera?

4. Nanga zotsatira zosapita kukayezetsa matenda limodzi pa nthawi yoyembekezera ndi chani?

22

Episode 5:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Kodi mumakonzekezera bwanji kubereka pamene muli oyembekezera?

3. Kodi chingachitike ndi chiyani ngati banja silinalkonzekere kubeleka?

4. Ndizofunika kuyamba liti kukonzekera kubereka?

Episode 6:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Ndi zofunika bwanji kudziwa masiku oyembekezera kubereka? Ubwino wake ndi otani?

3. Kodi mukudziwa kuti a chipatala amalimbikitsa kuti amayi oyembekezera akadikilire ku chipatala (ku chidikiro) pamene masiku obereka ayandikira?

4. Mukuona ngati ndi zofunika bwanji kudziwa masiku oyembekezera kubereka?

5. Inu mwakonzekera kapena munakonzekera bwanji kubereka?

6. Pali kuopsya kwanji koberekera kunyumba kapena mu njira yopita ku chipatala?

Episode 7:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Pali kuopsya kwanji koberekera kunyumba kapena mu njira yopita ku chiptala?

3. Kodi mukuona ngati imfa ya mwana wa Richard ndi Nasilina inakapewedwa bwanji? Makolo anakatani kupewa imfa ya mwanayu?

4. Inu mwakonzekera kapena munakonzera bwanji kubereka?

5. Inu pamene munali oyembekezera, mumadziwa tsiku lanu loyembekezera kubereka?

6. Kodi mutha kukwanitsa kukhala ku chidikiliro masiku anu obereka atayandikira?

7. Nthawi yabwino yokonzekera kukabereka mwana ku chipatala ndi iti?

23

8. Pa chikhulupiliro chanu, kodi mwana obadwa kumene amatengedwa ngati munthu? (A zakhali a nasilina akumukaniza kulira chifukwa maliro ndi a nchikuta; Kambiranani za kufunika kwa moyo wa mwana mokhudzana ndi maliro a m’chikuta)

Episode 8:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Ndaziona wangozindikira kumene kuti ali ndi mimba. Kodi mukuona ngati nthawi yabwino yoyamba sikelo ndi iti?

3. Kodi kupita kuchiptala nthawi yoyembekezera kapenanso mwana atabadwa, ndikofunika bwanji?

4. Mukudziwapo aliyense yemwe ananyalanyaza kupita ku sikelo? Zinawathera bwanji?

Episode 9:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Gama akunena kuti mwana wa Nasilina anamwalira chifukwa chakuti Esime wamulodza. Maganizo anu ndi otani pa zimenezi?

3. Mu dera lanu muli zikhulupiliro za makolo zotani zokhudzana ndi mimba, kapena ana obadwa kumene (ana a mchikuta)?

4. Mu dera lanu muli zikhulupiliro zotani zokhudzana ndi ana osakwana masiku?

5. Mukuona ngati zikhulupiliro zimenezi zimatengapo mbali yotani pa moyo kapena imfa ya ana osakwana masiku (zimalimbikitsa imfa kapena moyo wa anawa?)

24

Episode 10:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. A Namwino amulangiza Ndaziona kuti awonetsetse kuti wayendera ku sikelo kokwana kanayi pa nthawi yomwe ali oyembekezera. Inu munapita ku sikelo kangati pa nthawi yomwe munali ndi Mimba? Nanga munakumana ndi zophinja zotani pokwanitsa kupita ku sikelo kanayi konse?

3. Kuwonjezerapo pa zomwe zatchulidwa kale museweroli, kodi ndi zindikiro zina zoopsya ziti zofunika kuthamangira nazo ku chipatala pa nthawi yomwe mzimayi akuyembekezera?

4. Kodi moonjezera kanayi komwe mzimayi akuyenera kupita ku sikelo, ndi nthawi zina ziti zoyenera kuti apite ku chipatala?

Episode 11:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Mokhudzana ndi chi uchembere wabwino, kodi amayi oyembekezera azidya magulu angati a zakudya? Magulu ake a zakudya ndi ati?

3. Kodi ana osakwanamasiku akuyenera kulandira chisamaliro chotani?

4. Munamvako za Kangaroo? Mukudziwapo chiyani za kangaroo?

Episode 12:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Kuwonjezerapo pa zomwe zatchulidwa kale museweroli, kodi ndi zizindikiro zina zoopsya ziti zofunika kuthamangira nazo ku chitapala pa nthawi yomwe mzimayi akuyembekezera?

3. Kodi inu munamvako kapena kuonako zizindikiro ngati zimene zikukambidwa mu seweromu?

4. Inu munapanga kapena mutha kuchitapo chiyani kuti mupewe zizindikiro zimenezi?

5. Mukuona ngati chimachititsa zizindikiro zoopsya zimenezi ndi chiyani?

25

Episode 13:

Otsogolera Zokambirana: Ichi ndi chigawo chomaliza cha masewero a Khanda ndi Mphatso. Pali zambiri ndithu zomwe zikuchitika zokhudzana ndi Richard ndi Nasilina, komanso pakati pa Gibo, Mauluka ndi Ndaziona. Kodi Nasilina abwelera kwa Richard? Nanga Gibo zimuthera bwanji? Akhalabe omangidwa m’masamba choncho mosadziwa choona cheni cheni chomwe chikuchitika pakati pa Ndaziona ndi a Maluluka? Tcherani khutu kuti mumvetsere bwino bwino…

(Sewerani sewero lomaliza la nambala 13)

Otsogolera Zokambirana:

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Mukudziwapo chiyani za chisamaliro chomwe chimaperekedwa kwa ana osakwana masiku?

3. Ngati mukusamalira mwana wanu osakwana masiku munjira ya kangaroo pakali pano, zikuyenda bwanji? Mukukumana ndi zophinja zotani? Mukuona ngati mutha kuthananazo bwanji ziphinjozi?

4. Kodi ndi zotheka mwana osakwana masiku kukula ndi thanzi komanso nzeru?

5. Kodi mzimayi yemwe kale lonse sanaberekepo mwana osakwana masiku, athanso kubereka mwana osakwana masiku?

6. Ana osakwana masiku akuyenera kulandira chisamaliro chotani kuti akule ndi thanzi?

7. Munamvako za Kangaroo? Tiwuzeni za mbiri zokhudza kangaroo?

26

MUUNI WA KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA NYIMBO YA KHANDA NDI MPHATSO 5

Nyimbo ya Khanda ndi Mphatso inapangidwa mogwirizana ndi zolinga za kampeni, kuti ipititse patsogolo miyoyo ya ana ku Malawi. Nyimboyi inapangidwa kuti idziseweredwa pa wayilensi, ngakhalenso pa kanema. Imeneyi ndi nyimbo yachikondi yomwe kholo linayimbira mwana wake wakhanda okondedwa kusonyeza Chikondi chake.

Nyimboyi yakonsedwa kuti alangizi aKhanda ndi Mphatso akathe kuyisewera pena paliponse pomwe akukambirana ndi anthu kuphatikizapo mu chipatala, ku chidikiliro, ku sikelo ya amayi oyembekezera, mu zokambirana kapena zochitika zina ziri zonse za m’mudzi.

Nyimboyi mutha kuyisewera kuti anthu asangalare pamalo omwe mukuchita zochitika zokhudzana ndikampeni ya Khanda ndi Mphatso.

Munsimu muli mawu omwe ali mu nyimbo imeneyo ya Khanda ndi Mphatso omwe mungathe kuwatambusula pokambirana ndi anthu mukamaliza kuyisewera nyimboyi pa wayilesi kapena pa kanema.

27

ChorusKhanda ndi mphatso

Lipatseni mwayiKhanda ndi mphatso

Lipatseni mwayi

VerseMwana wanga ndidzakukonda ndi mtima wanga onse

Ndiwe duwa la pa mtima wangaSudzafota, nzakusamala nthawi zonseNdimakunyadira iwe mwana wanga

Ndidzakukupsopsona ine nthawi zonse mwanaweNdidzakuteteza ku zonse zowononga moyo

Ngati dzira nzakuchengeta mwana wanga iweyoNdidzakuchengeta ngati dzira mwanawe

Ndiwe mphatso yomwe anandipatsa YehovaNdiyamika Mulungu pondipatsa iweyo

VerseMmera mpoyamba ineyo ndikudziwaKukonzekera moyo ndi tsogolo lako ndinayamba ntangoima mwanaweBaby wanga ndiwe mphatso yanga

Mwana ndi mphatso, mphatso siichepa.Olo atachepa bwanji, mwana ndi mphatso basi

Mwayi okula ndi moyo wathanzi ndi nzeru Ndizakupatsa, iwe mwananga

Baby wanga ukaseka ine kumtima mbeee!Ukamadumphadumpha ine chimwemwe

Khanda Ndi Mpatso; Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana Za Nyimbo Ya Khanda Ndi Mphatso

1. Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?

2. Nyimboyi yakumvetsani motani? (funsani ngati yawasangalatsa, yawalimbikitsa, kapena yawakhumuditsa?)

3. Inu mukutha kulumikizananayo nyimboyi? Mukutha kuziona muli inu mu nyimboyi?

28

4. Mukuona ngati mawu oti: M’mera mpoyamba akutanthauza chiyani mu nyimboyi?

5. Munganenechiyani za mawu okuti: Khandi ndi Mphatso. Mukugwirizana nazo kapena ayi? Chifukwa chiyani?

6. Nanga mawu okuti: Khanda lingachepebwanji ndi mphatso basi Mukuwaona bwanji? Mukugwirizana nazo kapena ayi? Chifukwa chiyani?

7. Kodi khanda mungalipatse bwanji mwayi?

8. Mukuona ngati nyimboyi ikuonetsa zeni zeni zomwe makolo ambiri ku Malawi amakhalira ndi ana/makandaawo? Chifukwa chiyani?

9. Inu mutha kumva bwanji mutabereka mwana osakwana masiku?

10. Kanemayu akuonetsa mwana alipa Kangaroo, kodi zikuonetsa m’mene inu mumaganizira za Kangaroo? Chifukwa chiyani? Tifotokozereni m’mene mumaganizira za kangaroo?

11. Mutati mwapatsidwa mpata kukonzanso kanema ya nyimbo yaKhanda ndi Mphatso, mungayikonze bwanji? Mungayikemo zithunzi zotani? Chifukwa chiyani?

29

KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA KALENDALA YA UTHENGA WA CHISAMALIRO CHA ANA OSAKWANA MASIKU6

Kalendala yomwenso iri ndi uthenga ofunika osamalira ana osakwana masiku, yayikidwa mu phukusi limeneli kuti akathe kugawira anthu omwe akukambirana nawo, maka maka mabanja omwe abereka mwana osakwana masiku, ndipo akutulutsidwa kumene ku chipatala kuti akapitilize kusamalira mwana wao mu njira ya kangaroo kunyumba. Kalendalayi ikawathandizira makolowa kukumbukira zonse zofunika kuchita posamalira mwana wao, kuphatikizapo kukumbukira kubwereranso kuchipatala ndi mwana mogwirizana ndi malangizo a kuchipatala.

30

MALANGIZO OTHANDIZIRA KULANKHULANA NDI ANTHU7

Ngati mlangizi wa Khanda ndi Mphatso, mukhala mukulankhulana ndi anthu osiyana siyana pankhani zosamalira makanda, choncho ndizofunika kwambiri kuti mukhale ndi luso loyankhula bwino ndi anthu.

Ngati mukudziwa kuyankhula bwino ndi anthu, kumvera anthu komanso kutsogolera zokambirana ndi anthu, mutha kupititsa patsogolo uchembere wabwino komanso kupulumutsa miyoyo ya makanda ambiri mu dera lanu. Kulankhula bwino ndi anthu pankhani yokhudzana ndi umoyo kumapititsa patsogolo moyo wathanzi chifukwa anthu amamvetsetsa zomwe mukuwauza ndipo amatha kuchita zomwe mukunena.

Kulankhula ndi anthu ena aliwonse, kaya ndi pakati pa achipatala ndi anthu omwe abwera kuchipatala kuzafuna chitathindizo, kapena ndi anthu am’mudzi kapena mafumu amene, kumafunika kupatsana mpata okuti aliyense alankhuleko, osati munthu m’modzi yekha kumangolankhula yekha. Ndi zofunika kupereka mpata kwa mbali zonse kupereka maganizo awo kapena kufunsa pomwe sanamvetsetse.

31

1. Gwiritsani nthito chilankhulo chomveka bwino

2. Funsani mafunso oti anthu akhonza kuyankha chiri chonse chomwe angafune (monga Mukuganiza chiyani pankhaniyi), osati mafunso otsogolera komanso okuti anthu angoyankha kuti eya kapena ayi (monga ‘kodi nkhaniyi yakupangitsani kuti mukwiye?)

3. Onetsetsani kuti pasakhale chinthu china chiri chonse chokusokonezani pamene mukuyankhula ndi anthu (zinthu monga kuyankha foni)

4. Dziwanikuti thupi lanu limalankhula nawo ndipo anthu amatha kumva zambirikudzera mu zomwe likupanga thupi lanu. Onetsetsani kuti mayankhulidwe ndi machitidwe a thupi lanu akuonetsa Chikondi, umunthu ndi ulemu kwa anthu omwe mukuyankhula nawo.

5. perekani mpata kwa munthu yemwe akufotokoza nkhani yake, kuti anene momwe akumvera. Chonde mvetsetsani bwino ndipo onsetsani chidwi pomvetsera

6. Ngati muthu wakuuzani za nkhani yake, onetsetsani kuti muyimvetse nkhaniyo ndi kufunsisitsa monse moyenera kuti mumvetsetse bwino.

7. Pezani njira yoti muwalimbikitse anthu pamene agawana nanu nkhani yawo.

8. Onetsetsani kuti mwaona kuti zipangizo zonse zomwe ziri mu phukusi la alangizi aKhanda ndi Mphatso ziri bwino ndipo zikugwira ntchito yake bwino lomwe musanayambe kumvera kapena kugawirana ndi anthu omwe mukukambirana nawo. Mukhale ndi mpata ophunzira kagwiritsidwe ntchito ka zipangizo zonse musanayambe kugwira ntchito yopititsa patsogolo uchembere wabwino komanso kupulumutsa miyoyo ya makanda

M’munsimu muli zina mwa mfundo zomwe mungatsatire kuti mukalankhule bwino ndi anthu pogwira ntchito yopitsa patsogolo uchembere wabwino komanso kupulumutsa miyoyo ya makanda:

32

ZIPANGIZO ZINA 8M’munsimu mupeza zipangizo zina zoti zikuthandizireni kudziwa zambiri zokhudzana ndi uchembere wabwino, kupulumutsa miyoyo ya makanda, komanso kusamalira ana osakwana masiku mu njira ya kangaroo:

Care for the Small Baby

Kangaroo Mother Care Implementation Guide

March 2005

KANGAROO MOTHER CARE TRAINING MANUAL

SAVING NEWBORN LIVES

MALAWI

SAVE THE CHILDREN FEDERATION (USA)

March 31, 2005

Community Based Kangaroo Mother Care (CKMC) Training Manual For CKMC Trainers, Supervisors and Community Workers

Mmene Tingasamalire Ndi Kukutira Khanda Lobadwa Masiku Asanakwane

Small Baby Care (Bina Power Point)

Kangaroo Mother Care: A Practical Guide

KMC Training Manual (SNL 2005)

MCHIP KMC Guide (2012)

MCHIP KMC Guide (2012)

33

ZAMBIRI ZOKHUDZANA NDI UCHEMBERE WABWINO, UMOYO WA MAKANDA NDI CHISAMALIRO CHA ANA OSAKWANA MASIKU 9

Munsimu mupeza zambiri zokhudzana ndi uchembere wabwino, unoyo wa thanzi wa makanda komanso chisamaliro chaana osakwanamasiku. Izi zikuthandizani kuti mukathe kupereka uthenga ofunikira kwa anthu omwe mukukambirana nawo zokhudza Khanda ndi Mphatso.

Chisamaliro cha ana osakwana masiku

Chisamaliro cha amayi oyembekezera

Kukonzekera kuchira kwabwino

• Akuyenera kudya zakudya zakasinthasintha zochokera ku magulu 6 azakudya pafupipafupi komanso mokwanira

• Akhale aukhondo pathupi pawo, panyumba pawo komanso pazakudya zonse.

• APite ku sikelo ya amayi oyembekezera pamodzi ndi mamuna wake kosachepera kanayi kuyambira pamene wazindikira kuti ali ndi mimba kuti akalandire uphungu ndi chithandizo choyenelera mokwanira ndi mwachangu.

• Ayenera kuyezedwa ngati ali ndi HIV, malungo, matenda a chindoko, kuthamanga magazi ndi matenda ena. Ndikuthandizidwa moyenera ngati apezedwa ndi matenda ali onse

• Alandire mankhwala a malungo, a njoka za mmimba ndi oonjezera magazi.

• Atetezedwe kumatenda a malungo pogona mu net usiku ulionse tsiku lili lonse

• Azikhala ndi nthawi yopuma yokwanira (Adzipumula mokwanira kosachepera ola limodzi masana komanso maola 6 kapena 8 usiku

• Apewe ntchito zolemetsa monga kunyamula katundu wolemera

• Adzimwa madzi a ukhondo pafupi pafupi

• Kukonzekera za kubadwa kwa mwana komanso vuto lililonse lomwe lingadze.

Dziwani zizindikiro zokuti nthawi yobereka yafika ndi zizindikiro zoopsya kwa amayi oyembekezera

34

• Sungani ndalama zozagwiritsa ntchito pa ulendo okabereka ku chipatala

• Konzekeranitu za momwe mudzayendere kupitakukachira ku chipatala pa nthawi yake kapenanso ngati zovuta zina zitagwa mwadzidzi

• Sankhani nzanu kapena wachibale amene angadzakuthandizeni kupita ku chipatala, ndi wina amene angadzakusamalireni ana kunyumba

• Konzekerani zokakhalaku chidikiliro nthayi yabwino

• Pezeranitu zovala ndi zofunda za mwana zosamalika bwino

Ubwino opita kusikelo motsatila ndondomeko pamene amayi ali oyembekezera

Ubwino wa abambo kupita limodzi ndi amayi ku sikelo

• Pezeranitu lezala la nyuwani la pangozi ndi kulisunga mosamala

• Mayi amalandira zithandizo zonse moyenera ndi mokwanira bwino ngati atsatira ndondomeko yasikelo komanso kuyamba sikelo mmiyezi itatu yoyamba.

• Thanzi la mayi ndi mwana oyembekezeredwa limapimidwa pafupipafupi.

• Mayi amathandizidwa moyenera pavuto lililonse limene ladza kuti mwana obadwayo akhale wathanzi.

• Amaphunzitsidwa ndi kulimbikitsidwa kukhala moyo wathanzi poyembekezera mwana

• Amakonzekeretsedwa za chisamaliro cha mwana ngakhale mwanayo atabadwa masiku osakwana.

• Amalandira makatemera onse mwandondomeko omwe amathandizira kupewa matenda kwa mayi ndi mwana obadwayo monga katemera wa kafumbata

• Amalandira mankhwala a SP oteteza malungo

• Amalandira mankhwala owonjezera magazi ndi Vitamin A omwe amathandiza kupewa matenda ndi mavuto ena a uchembere

• Bambo ndi mayi amalangizidwa pamodzi zakukhala moyo wathanzi panthawi ya mimba.

• Bambo amamvetsetsa za momwe thanzi la mayi limayendera panthawi ya mimba ndipo ndikosavuta kupangira limodzi dongosolo la banja lawo limodzi makamaka pa family planning (planning the family)

35

• Abambo amazindikira za zofunikira za uchembere wabwino ndipo amapereka chithandizo chokwanira kwa mayi ndi mwana obadwayo

Kupita ku sikelo mwachangu ndi mwandondomeko ndi kutsatira malangizo onse.

Zinthu zofunikira kwambiri kuzidziwa banja likakhala loyembekezera

Udindo wa achibale kwa amayi oyembekezera kuti akhale ndi thanzi

Zizindikiro zoopsya kwa amayi oyembekezera

• Kuzindikira mavuto adzidzidzi ndi kuchitapo kanthu mwamsanga

• Alimbikitse mayi kupita kusikelo munthawi yoyenra

• Akonzekere kuthandiza mayi ntchito zolemetsa zapakhomo.

• Kukonzekera za kupeza chithandizo chakuchipatala pamene chafunikirapo ngakhale mwadzidzidzi.

• Kuthandizira kukonza zakudya zakasinthasintha kwa mayi oyembekezera.

• Kupereka zofunikira zonse mwanayo atabadwa masiku osakwana

Mayi aliyense oyembekezera ali pa chiopsyezo. Dziwani zizindikiro zoopsyakwa mayi wapakati ndipo khalani okonzeka kupitaku chipatala msanga mukaona zizndikirozi.

Zizindikiro zokuti matenda ayamba kwa amayi oyembekezera

• Kutaya magazi kapena madzi ku maliseche

• Kupweteka pansi pa mchombo ndi nsana

• Kupotokola kwa m’mimba pafupi pafupi (pa mphindi 20 ziri zones kapena pamphindi zochepera apo)

Amayi oyembekezera akuyenera kuthamangira ku chipatala akaona zindikiro zimenezi

Zizindikiro zosonyezakuti pali vuto linalake ndi mimba

• Kuyera lilime ndi zikope

• Kumva kutopa ndi kubanika

• Kutupikanakwa miyendo,manja ndi nkhope

• Mwana osamveka kugunda m’mimba

36

Zizindikiro zoopsya. Pitani nsanga ku chipatala mukaona zizindikiro izi:

• Kumva kupweteka kwambiri mutu kapena kuchita chidima

• Kutentha thupi ndi kufooka

• Kupuma mofulumira kapena movutikira

• Kupweteka m’mimba kwambiri

• Kumva kutopa

• Kutaya magazi ku maliseche

• Kukomoka

Zinthu zimene zimapangitsa kuti mayi abereke masiku asanakwane

Ndi ndani amene angabereke mwana osakwana masiku?

Kangaroo ndi chiyani?

• Ngakhale popanda chifukwa chirichonse mayi akhoza kubereka masiku asankwane.

• Matenda omwe adza mthupi lamayi omwe amakakhudzanso mwana mmimba monga malungo.

• Mimba yamapasa chifukwa chakuchepa kwa malo mchiberekero

Chofunikira kwambiri ndi kuyamba kupita ku sikelo pamene mayi wazindikira kuti ali ndi mimba kuti akapatsidwe uphungu ndi chithandizo choyenelera.

Mzimayi wina aliyense atha kubereka mwana osakwana masiku. Sizikuthanthauza kuti amene amabeleka mwana osakwana masiku ndi olakwa, zitha kuchitikira wina aliyense.

• Ndi chisamaliro chopatsidwa kwa mwana obadwa masiku osakwana chimene mwana amayikidwa pa chifuwa pakholo lake kuti alandire kutentha, chakudya, chitetezo kuti ziwalo zake zikhwime.

• Mwanayu amabadwa ziwalo zonse zosakhwima ndipo afunika kupatsidwa kutentha, chakudya, chitetezo potsatira njira ya kangaroo.

• Mwana akangobadwa amayikidwa pachifuwa cha kholo lake kuti thupi lawo ligundane ndikugawana kutentha.

37

• Mwana osakwana masiku amafunika:

» Kumuthandizira kudyetsedwa mkaka wa mmawere.

» Kumuyang’anira ndi kumuyeza pafupipafupi.

Ubwino wogwritsa njira ya kangaroo kwa mwana obadwa masiku osakwana

• Mwana amalandira chifundizi chokwanira nthawi zonse.

• Mwana amadyetsedwa mokwanira

• Imalimbikitsa Chikondi cha kholo pa mwana.

• Mwana amatetezedwa kumatenda ndi mavuto osiyanasiyana.

• Amatulutsidwa msanga kuchipatala chifukwa mwana amakwaniritsa msanga zifukwa zotulutsidwira mwachangu choncho amatha kusamalira zina zapakhomo.

Udindo wa abambo pothandiza kusamalira mwana osakwana masiku

• Kupereka chilimbikitso

• Kupereka zonse zofunika posamalira mwanayo

• Kuthandizira ntchito zapakhomo.

• Kuyika mwana pachifuwa (kangaroo)

• Kuthandizira kubwereranso kuchipatala monga kwafunikira.

Udindo wa abale ndi anthu ena a mmudzi pothandiza kusamalira mwana osakwana masiku

• Kupereka chilimbikitso kwa banjali

• Kuthandiza ntchito zapakhomo

• Kuthandizira kubwereranso kuchipatala monga kwafunikira.

• Kuthandizira zofunikira pachithandizo cha mwana.

• Kuthandizira kusamalira mwana pomuyikapa kangaroo

38

Nthawi zoyenera kubweranso kuchipatala pamene mukusamala mwana pa kangaroo kunyumba?

Pitani kuchipatala tsiku limene madotolo anakulangizani.

Thamangirani kuchipatala ngati mwaona vuto lilironse ngakhale tsiku lobwereranso kuchipatala silinafike.

Mavuto oyenera kuthamangira naye mwana kuchipatala mwachangu

• Kutentha thupi.

• Kukomoka

• Chikasu

• Kupuma movutikira/mobanika

• Kufooka

• Kukanika kuyamwa

• Kufiira, kutupa ndi mafinya pamchombo

• Kalikonse kovuta komwe kakudabwitsani pa mwana

40

Cholinga cha bukhuli ndi kuwunikira alangizi kagwiritsidwe ntchito ka Phukusipa la zipangizo za alangizi a Khanda ndi Mphatso. Phukusili lapangidwa kuti lithandzire alangizi a khanda ndi Mphatso kugwira ntchito yopititsa patsogolo moyo wamakanda mu dera lawo, kudzera mu zokambirana ndi anthu. Zokambiranazi cholinga chake ndi kupititsa patsogolo moyo wathanzi wa amayi ammimba ndi makanda, komanso kudziwitsa anthu zambiri za ubwino wosamalira ana osakwana masiku mu njira ya Kangaroo. Cholinga cha phukusili maka maka ndikuthandzira kuti anthu atengepo mbali polimbana ndi ziphinjo zosiyana siyana zomwe zimapititsa pansi miyoyo ya makanda, maka maka osakwana masiku. Ndi cholinga cha phukusili kusintha zikhalidwe ndi zikhulupiro, komanso kulimbikitsa abambo kuti atenge nawo mbali posamalira moyo wa amayi a mimba ndi makanda.

Phukusili liri ndi zipangizo zisanu ndi ziwiri (7) zomwe ziri ndi nkhani ndi uthenga okhudzana ndi uchembere wabwino, moyo wa thanzi wa makanda komanso chisamaliro cha Kangaroo kwa ana osakwanamasiku:

˝ Flipchart yophunzitsira za Kangaroo

˝ Khani za Chiyembekezo zolimbikitsa Kangaroo

˝ Masewero a Khanda ndi Mphatso

˝ Nyimbo ya Khanda ndi Mphatso (ya pa wayilesi ndi kanema)

˝ Uthenga wa Khanda ndi Mphatso (radio spots)

˝ Kalendala ya Khanda ndi Mphatso

˝ Muuni wa kagwiritsidwe ntchito kaphukusi la alangizi aKhanda ndi

Bukhuli ndi chowunikira/muuni wolozera m’mene chipangizo chiri chonse chingagwiritsidwire ntchito pokambirana za uchembere wabwino ndi umoyo wa makanda ndi anthu osiyana siyana.

Phukusi la alangizi a Khanda ndi Mphatso linapangidwa ndi Unduna wa zaumoyo mogwirizana ndi bungwe Save the Children , pamodzi ndi anthu ndi mabungwe ena monga Mercantile International, ADECOTS, ndi Center for Development Communication. Cholinga cha phukusili ndi kuthandizira kupititsa patsogolo uchembere wabwino komanso umoyo wa makandaku Malawi.